6 nati, Yehova Mulungu wa makolo athu, Inu sindinu Mulungu wa m'Mwamba kodi? sindinu woweruza maufumu onse a amitundu kodi? ndi m'dzanja mwanu muli mphamvu yolimba; palibe wina wakulaka Inu.
7 Sindinu Mulungu wathu, amene munainga nzika za m'dziko muno pa maso pa ana anu Israyeli, ndi kulininkha kwa mbeu ya Abrahamu bwenzi lanu kosatha?
8 nakhala m'mwemo iwowa, nakumangirani m'mwemo malo opatulika a dzina lanu, ndi kuti,
9 Cikatigwera coipa, lupanga, ciweruzo, kapena mliri, kapena njala, tidzakhala ciriri pakhomo pa nyumba iyi, ndi pamaso panu, (pakuti m'nyumba muno muli dzina lanu), ndi kupfuulira kwa Inu m'kusauka kwathu; ndipo mudzamvera ndi kulanditsa.
10 Ndipo tsopano, taonani ana a Amoni, ndi Moabu, ndi a ku phiri la Seiri, amene simunalola Israyeli awalowere, pakuturuka iwo m'dziko la Aigupto, koma anawapambukira osawaononga;
11 tapenyani, m'mene atibwezera; kudzatiinga m'colowa canu, cimene munatipatsa cikhale colowa cathu.
12 Mulungu wathu, simudzawaweruza? pakuti mwa ife mulibe mphamvu yakulimbana nao aunyinji ambiri awa akutidzera; ndipo sitidziwa ngati tidzatani, koma maso athu ali kwa Inu.