10 Ndipo akalonga onse ndi anthu onse anakondwera, nabwera nazo, naponya m'bokosi mpaka atatha.
11 Ndipo kunali, pamene amabwera nalo bokosi alipenye mfumu, mwa manja a Alevi, nakapenya kuti ndalama zinacurukamo, amadza mlembi wa mfumu, ndi kapitao wa wansembe wamkulu, nakhutula za m'bokosi, nalisenza ndi kubwera nalo kumalo kwace. Anatero tsiku ndi tsiku, nasonkhanitsa ndalama zocuruka.
12 Ndipo mfumu ndi Yehoyada anazipereka kwa iwo akugwira nchito ya utumiki ya nyumba ya Yehova, nalembera amisiri omanga ndi miyala, ndi osema mitengo, akonzenso nyumba ya Yehova; ndiponso akucita ndi citsulo ndi mkuwa alimbitse nyumba ya Yehova.
13 Momwemo anacita ogwira nchito, nikula nchito mwa dzanja lao, nakhazikitsa iwo nyumba ya Mulungu monga mwa maonekedwe ace, nailimbitsa.
14 Ndipo ataitsiriza, anabwera nazo ndalama zotsala kwa mfumu ndi Yehoyada, napanga nazo zipangizo za nyumba ya Yehova, zipangizo za kutumikira nazo, ndi kupereka nsembe nazo, ndi zipande, ndi zipangizo za golidi ndi siliva. Ndipo anapereka kosalekeza nsembe zopsereza m'nyumba ya Yehova masiku onse a Yehoyada.
15 Koma Yehoyada anakalamba, nacuruka masiku, namwalira iye; ndiye wa zaka zana limodzi mphambu makumi atatu pamene anamwalira.
16 Ndipo anamuika m'mudzi wa Davide, pakati pa mafumu; pakuti anacita zabwino m'Israyeli, ndi kwa Mulungu, ndi ku nyumba yace.