1 Amaziya anali wa zaka makumi awiri mphambu zisanu polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zinai; ndi dzina la mace ndiye Yehoadana wa ku Yerusalemu.
2 Ndipo anacita zoongoka pamaso pa Yehova, koma wosacita ndi mtima wangwiro.
3 Kunacitika tsono, utamkhazikikira ufumu, anapha anyamata ace amene adapha mfumu atate wace.
4 Koma sanapha ana ao, koma anacita monga umo mulembedwa m'cilamulo, m'buku la Mose, monga Yehova analamulira, ndi kuti, Atate asafere ana, ndi ana asafere atate; koma yense afere chimo lace lace.
5 Ndipo Amaziya anamemeza Ayuda, nawaika monga mwa nyumba za atate ao, atsogoleri a zikwi, ndi atsogoleri a mazana, ndiwo onse a Yuda ndi Benjamini; nawawerenga a zaka makumi awiri ndi mphambu, nawapeza amuna osankhika zikwi mazana atatu akuturukira kunkhondo, ogwira mkondo ndi cikopa.