1 Yotamu anali wa zaka makumi awiri, mphambu zisanu polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka khumi ndi zisanu ndi cimodzi; ndi dzina la mace ndiye Yerusa mwana wa Zadoki.
2 Ndipo anacita zoongoka pamaso pa Yehova, monga umo adacitira atate wace Uziya; pokhapo sanalowa m'Kacisi wa Yehova. Koma anthu anacitabe zobvunda.
3 Anamanga cipata ca kumtunda ca nyumba ya Yehova, ndi pa linga la Ofeli anamanga kwakukuru.
4 Namanga midzi m'mapiri a Yuda, ndi m'nkhalango anamanga nyumba zansanja, ndi nsanja zomwe.