2 Ndipo anacita zoongoka pamaso pa Yehova, monga umo adacitira atate wace Uziya; pokhapo sanalowa m'Kacisi wa Yehova. Koma anthu anacitabe zobvunda.
3 Anamanga cipata ca kumtunda ca nyumba ya Yehova, ndi pa linga la Ofeli anamanga kwakukuru.
4 Namanga midzi m'mapiri a Yuda, ndi m'nkhalango anamanga nyumba zansanja, ndi nsanja zomwe.
5 Anayambananso ndi mfumu ya ana a Amoni, namgonjetsa, Ndi ana a Amoni anamninkha caka comweci matalente a siliva zana limodzi, ndi miyeso ya tirigu zikwi khumi, ndi ya barele zikwi khumi. Ana a Amoni anabwera nazo zomwezo kwa iye caka caciwiri ndi cacitatu comwe.
6 Momwemo Yotamu anakula mphamvu, popeza anakonza njira zace pamaso pa Yehova Mulungu wace.
7 Macitidwe ena tsono a Yotamu, ndi nkhondo zace zonse, ndi njira zace, taonani, zalembedwa m'buku la mafumu a Israyeli ndi Yuda.
8 Anali wa zaka makumi awiri mphambu zisanu polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka khumi mphambu zisanu ndi cimodzi.