1 Ahazi anali wa zaka makumi awiri polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka khumi mphambu zisanu ndi cimodzi; koma sanacita zoongoka pamaso pa Yehova ngati Davide kholo lace,
2 koma anayenda m'njira za mafumu a Israyeli, napangiranso Abaala mafano oyenga,
3 Nafukizanso yekha m'cigwa ca mwana wa Hinomu, napsereza ana ace m'moto, monga mwa zonyansa za amitundu, amene Yehova anawainga pamaso pa ana a Israyeli.
4 Naphera nsembe, nafukiza kumisanje, ndi kuzitunda, ndi patsinde pa mtengo uli wonse wogudira.
5 Cifukwa cace Yehova Mulungu wace anampereka m'dzanja la mfumu ya Aramu; ndipo anamkantha, natenga ndende unyinji waukuru wa anthu ace, nafika nao ku Damasiko. Anaperekedwanso iye m'dzanja la mfumu ya Israyeli, amene anamkantha makanthidwe akuru.
6 Pakuti Peka mwana wa Remaliya anapha ku Yuda tsiku limodzi zikwi zana limodzi ndi makumi awiri, ngwazi zonsezo; popeza adasiya Yehova Mulungu wa makolo ao.
7 Ndipo Zikiri munthu wamphamvu wa Efraimu anapha Maseya mwana wa mfumu, ndi Azrikamu woyang'anira nyumba, ndi Elikana wotsatana ndi mfumu.