26 Alevi tsono anaimirira ndi zoyimbira za Davide, ndi ansembe anakhala ndi malipenga.
27 Nanena Hezekiya kuti apereke nsembe yopsereza pa guwa la nsembe. Ndipo pakuyamba nsembe yopsereza, inayambanso nyimbo ya Yehova ndi malipenga, pamodzi ndi zoyimbira za Davideyo mfumu ya Israyeli.
28 Ndi msonkhano wonse unalambira, ndi oyimbira anayimba, ndi amalipenga anaomba; zonsezi mpaka adatsiriza nsembe yopsereza.
29 Ndipo atatsiriza kuperekaku, mfumu ndi onse opezeka pamodzi naye anawerama, nalambira.
30 Hezekiya mfumu ndi akalonga anauzanso Alevi ayimbire Yehova zomlemekeza ndi mau a Davide ndi a Asafu mlauli. Ndipo anayimbira zomlemekeza mokondwera, nawerama mitu yao, nalambira.
31 Pamenepo Hezekiya anayankha, nati, Tsopano mwadzipatulira kwa Yehova, senderani, bwerani nazo nsembe zophera ndi nsembe zoyamika ku nyumba ya Yehova. Ndi msonkhano unabwera nazo nsembe zophera ndi nsembe zoyamika, ndi onse a mtima wofuna mwini anabwera nazo nsembe zopsereza.
32 Ndi kuwerenga kwace kwa nsembe zopsereza unabwera nazo msonkhanowo ndiko ng'ombe makumi asanu ndi awiri, nkhosa zamphongo zana limodzi, ndi ana a nkhosa mazana awiri; zonsezi nza nsembe yopsereza ya Yehova.