14 Ndi uti mwa milungu yonse ya mitunduyi ya anthu, amene makolo anga anawaononga konse, unakhoza kulanditsa anthu ace m'dzanja mwanga, kuti Mulungu wako adzakhoza kukulanditsa iwe m'dzanja mwanga?
15 Ndipo tsono, asakunyengeni Hezekiya, ndi kukukopani motero, musamkhulupirira; pakuti palibe mulungu wa mtundu uli wonse wa anthu, kapena ufumu uli wonse, unakhoza kulanditsa anthu ace m'dzanja mwanga; ndipo kodi Mulungu wanu adzakulanditsani inu m'dzanja langa?
16 Ndipo anyamata ace anaonjeza kunena motsutsana ndi Yehova Mulungu, ndi mnyamata wace Hezekiya,
17 Analemberanso akalata a kunyoza Yehova Mulungu wa Israyeli, ndi kunena motsutsana ndi Iye, ndi kuti, Monga milungu ya mitundu ya anthu a m'maiko, imene siinalanditsa anthu ao m'dzanja langa, momwemo Mulungu wa Hezekiya sadzalanditsa anthu ace m'dzanja mwanga.
18 Ndipo anapfuula ndi mau akuru m'cinenedwe ca Ayuda kwa anthu a m'Yerusalemu okhala palinga, kuwaopsa ndi kuwabvuta, kuti alande mudziwu.
19 Nanenera Mulungu wa Yerusalemu, monga umo amanenera milungu ya mitundu ya anthu a pa dziko lapansi, ndiyo nchito ya manja a anthu.
20 Ndipo Hezekiya mfumu, ndi Yesaya mneneri mwana wa Amozi, anapemphera pa ici, napfuulira Kumwamba.