6 Naika akazembe a nkhondo alamulire anthu, nawasonkhanitsira kuli iye ku bwalo la ku cipata ca mudzi, nanena nao motonthoza mtima wao ndi kuti,
7 Limbani, mulimbike mtima, musaopa kapena ku tenga nkhawa pankhope pa mfumu ya Asuri ndi aunyinji okhala naye; pakuti okhala nafe acuruka koposa okhala naye;
8 pamodzi ndi iye pali dzanja la thupi lanyama; koma pamodzi ndi ife pali Yehova Mulungu wathu, kutithandiza ndi kutigwirira nkhondo. Ndipo anthu anacirikizika ndi mau a Hezekiya mfumu ya Yuda.
9 Pambuyo pace Sanakeribu mfumu ya Asuri, akali ku Lakisi ndi mphamvu yace yonse pamodzi naye, anatuma anyamata kwa Hezekiya mfumu ya Yuda, ndi kwa Ayuda onse okhala ku Yerusalemu, ndi kuti,
10 Atero Sanakeribu mfumu ya Asuri, Mutama ciani kuti mukhala m'linga m'Yerusalemu?
11 Sakukopani Hezekiya, kuti akuperekeni mufe nayo njala ndi ludzu, ndi kuti, Yehova Mulungu wathu adzatilanditsa m'dzanja la mfumu ya Asuri?
12 Sanaicotsa misanje yace ndi maguwa ace a nsembe Hezekiya yemweyo, nauza Yuda ndi Yerusalemu, ndi kuti, Mugwadire ku guwa la nsembe limodzi ndi kufukiza zonunkhira pamenepo?