21 Amoni ndiye wa zaka makumi awiri mphambu ziwiri polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka ziwiri.
22 Ndipo anacita coipa pamaso pa Yehova, monga umo anacitira Manase atate wace; pakuti Amoni anaphera nsembe mafano osema onse amene adawapanga Manase atate wace, nawatumikira.
23 Koma sanadzicepetsa pamaso pa Yehova, monga umo anadzicepetsera Manase atate wace; koma Amoni amene anacurukitsa kuparamula kwace.
24 Ndipo anyamata ace anampangira ciwembu, namupha m'nyumba yace yace.
25 Koma anthu a m'dziko anapha onse adampangira ciwembu mfumu Amoni; ndi anthu a m'dziko analonga Yosiya mwana wace akhale mfumu m'malo mwace.