4 Namanga maguwa a nsembe m'nyumba ya Yehova, imene Yehova adati, M'Yerusalemu mudzakhala dzina langa ku nthawi zonse.
5 Namangiranso khamu lonse la kuthambo maguwa a nsembe m'mabwalo awiri a nyumba ya Yehoya.
6 Anapititsanso ana ace pamoto m'cigwa ca ana a Hinomu, naombeza maula, nasamalira malodza, nacita zanyanga, naika obwebweta ndi openduza; anacita zoipa zambiri pamaso pa Yehova kuutsa mkwiyo wace.
7 Ndipo anaika cifanizo cosema ca fanolo adacipanga m'nyumba ya Mulungu, imene Mulungu adati kwa Davide ndi Solomo mwana wace, M'nyumba muno ndi m'Yerusalemu umene ndausankha m'mafuko onse a Israyeli ndidzaika dzina langa ku nthawi zonse;
8 ndipo sindidzasunthanso phazi la Israyeli ku dziko ndaliikira makolo anu; pokhapo asamalire kucita zonse ndawalamulira, cilamulo conse, ndi malemba, ndi maweruzo, mwa dzanja la Mose.
9 Koma Manase analakwitsa Yuda ndi okhala m'Yerusalemu, kotero kuti anacita coipa koposa amitundu, amene Yehova anawaononga pamaso pa ana a Israyeli.
10 Ndipo Yehova analankhula ndi Manase ndi anthu ace, koma sanasamalira.