3 Ndi pansi pace panali mafanziro a ng'ombe zakulizinga khumi ku mkono umodzi, zakuzinga thawalelo pozungulira pace. Ng'ombezo zinali m'mizere iwiri, zinayengeka poyengedwa thawalelo.
4 Linasanjikika pa ng'ombe khumi ndi ziwiri, zitatu zinapenya kumpoto, ndi zitatu zinapenya kumadzulo, ndi zitatu zinapenya kumwela, ndi zitatu zinapenya kum'mawa; ndi thawale linasanjikika pamwamba pao, ndi nkholo zao zinayang'anana.
5 Ndi kucindikira kwace kunanga cikhato, ndi mlomo wace unasadamuka ngati mlomo wa comwera, ngati luwa la kakombo; analowamo madzi a mitsuko yaikuru zikwi zitatu.
6 Anapanganso mbiya zamphwamphwa khumi, naika zisanu ku dzanja lamanja, ndi zisanu ku dzanja lamanzere, kutsukiramo; za nsembe yopsereza anazitsuka m'menemo; koma thawale ndi la ansembe kusambiramo.
7 Ndipo anapanga zoikapo nyali khumi zagolidi, monga mwa ciweruzo cace; naziika m'Kacisi, zisanu ku dzanja lamanja, ndi zisanu ku dzanja lamanzere.
8 Anapanganso magome khumi, nawaika m'Kacisi, asanu ku dzanja lamanja, ndi asanu ku dzanja lamanzere. Napanga mbale zowazira zana limodzi zagolidi.
9 Anamanganso bwalo la ansembe, ndi bwalo lalikuru, ndi zitseko za kubwalo, nakuta zitseko zace ndi mkuwa.