12 Pamenepo Solomo anapereka nsembe zopsereza kwa Yehova pa guwa la nsembe la Yehova, limene adalimanga pakhomo palikole,
13 monga momwe mudayenera, tsiku ndi tsiku; napereka monga momwe adauza Mose pamasabata, pokhala mwezi, ndi pa madyerero oikika, katatu m'caka, pa madyerero ali mkate wopanda cotupitsa, ndi pa madyerero a masabata, ndi pa madyerero a misasa.
14 Ndipo anaika monga mwa ciweruzo ca Davide atate wace zigawo za ansembe ku utumiki wao, ndi Alevi ku udikiro wao, kulemekeza Mulungu, ndi kutumikira pamaso pa ansembe, monga munayenera tsiku ndi tsiku; odikira omwe monga mwa zigawo zao ku cipata ciri conse; pakuti momwemo Davide munthu wa Mulungu adamuuza.
15 Ndipo sanapambuka pa lamulo la mfumu la kwa ansembe ndi Alevi, kunena za kanthu kali konse, kapena za cumaci.
16 Momwemo nchito yonse ya Solomo inakonzekeratu tsiku lakuika maziko a nyumba ya Yehova, mpaka anaitsiriza.
17 Pamenepo Solomo anamuka ku Ezioni Geberi, ndi ku Eloti pambali pa nyanja, m'dziko la Edomu.
18 Ndipo Huramu anamtumizira zombo, ndi amarinyero ace, ndi anyamata akudziwa za m'nyanja; ndipo anamuka pamodzi ndi anyamata a Solomo ku Ofiri, natengako matalente mazana anai mphambu makumi asanu a golidi, nabwera nao kwa Solomo mfumu.