28 pakuti mwa iye tikhala ndi moyo ndi kuyendayenda, ndi kupeza mkhalidwe wathu; monga enanso a akuyimba anu ati, Pakuti ifenso tiri mbadwa zace.
29 Popeza tsono tiri mbadwa za Mulungu, sitiyenera kulingalira kuti umulungu uli wofanafana ndi golidi, kapena siliva, kapena mwala, woloca ndi luso ndi zolingalira za anthu.
30 Nthawi za kusadziwako tsono Mulungu analekerera; koma tsopanotu alinkulamulira anthu onse ponse ponse atembenuke mtima;
31 cifukwa anapangira tsiku limene adzaweruza dziko lokhalamo anthu m'cilungamo, ndi munthu amene anamuikiratu; napatsa anthu onse citsimikizo, pamene anamuukitsa iye kwa akufa.
32 Ndipo pamene anamva za kuuka kwa akufa ena anaseka pwepwete; koma ena anati, Tidzakumvanso za cimeneci.
33 Conco Paulo anaturuka pakati pao.
34 Koma ena anadziphatika kwa iye, nakhulupira; mwa iwonso munali Dionisiyo Mareopagi, ndi mkazi dzina lace Damarisi, ndi ena pamodzi nao.