15 Ndipo atatu a akuru makumi atatu anatsikira kuthanthwe kwa Davide, ku phanga la Adulamu; ndi nkhondo ya Afilisti idamanga misasa m'cigwa ca Refaimu.
16 Pamenepo Davide anali m'linga, ndi boma la askari linali ku Betelehemu.
17 Ndipo Davide analakalaka, nati, Ha! mwenzi wina atandimwetsa madzi a m'citsime ca ku Betelehemu ciri kucipata,
18 Napyola atatuwo misasa ya Afilish natunga madzi ku citsime ca ku Betelehemu ciri kucipata, nabwera nao kwa Davide; koma Davide anakana kumwako, koma anawathirira kwa Yehova;
19 nati, Pali Mulungu wanga, kukhale kutali kwa ine kucita ici. Ngati ndidzamwa mwazi wa anthu awa? Akadataya moyo wao, inde akadataya moyo wao, pakukatenga madziwa. M'mwemo sanafuna kuwamwa. Izi anazicita atatu amphamvuwa.
20 Ndipo Abisai mbale wa Yoabu, ndiye wamkuru wa atatuwa; pakuti anasamulira mazana atatu mkondo wace, nawapha, namveka dzina pakati pa atatuwa.
21 Mwa atatuwa iye anali waulemu woposa awiriwa, nasanduka mkuru wao; koma sanafikana nao atatu oyamba aja.