9 Ndipo Davide anakula-kulabe, pakuti Yehova wa makamu anali naye.
10 Akuru a amphamvu aja Davide anali nao akulimbika pamodzi naye m'ufumu wace, pamodzi ndi Aisrayeli onse, kumlonga ufumu, monga mwa mau a Yehova akunena za Israyeli, ndi awa.
11 Kuwerenga kwa amphamvu aja Davide anali nao ndi uku: Yasobeamu mwana wa Mhakimoni, mkuru wa makumi atatu aja, anasamulira mazana atatu mkondo wace, nawapha nthawi imodzi.
12 Ndi pambuyo pace Eleazara mwana wa Dodo M-ahohi, ndiye mmodzi wa atatu aja amphamvu.
13 Anali pamodzi ndi Da vide ku Pasidamimu muja; Afilisti anasonkhanako kunkhondo kumene kunali munda wodzala ndi barele; ndipo anthu anathawa pamaso pa Afilisti.
14 Koma anadziimika pakati pa munda, naulanditsa, nakantha Afilisti; m'mwemo anawapulumutsa Yehova ndi cipulumutso cacikuru.
15 Ndipo atatu a akuru makumi atatu anatsikira kuthanthwe kwa Davide, ku phanga la Adulamu; ndi nkhondo ya Afilisti idamanga misasa m'cigwa ca Refaimu.