18 Ndipo iye anati, Mumkomere mtima mdzakazi wanu. Comweco mkaziyo anamuka, nakadya, ndi nkhope yace siinakhalanso yacisoni.
19 Ndipo iwo anauka mamawa, nalambira pamaso pa Yehova, nabwerera, nafikanso kwao ku Rama; ndipo Elikana anadziwa mkazi wace Hana, Yehova namkumbukila iye.
20 Ndipo panali pamene nthawi yace inafika, Hana anaima, nabala mwana wamwamuna: namucha dzina lace Samueli, nati, Cifukwa ndinampempha kwa Yehova,
21 Ndipo munthuyo Elikana, ndi a pa banja lace onse, anakwera kukapereka kwa Yehova nsembe ya caka ndi caka, ndi ya cowinda cace.
22 Koma Hana sadakwera, cifukwa kuti anati kwa mwamuna wace, Sindidzakwerako kufikira mwanayo ataleka kuyamwa, pamenepo ndidzapita naye kuti aoneke pamaso pa Yehova, ndi kukhalako cikhalire.
23 Ndipo Elikana mwamuna wace anati, Cita cimene cikukomera nukhale kufikira utamletsa kuyamwa; komatu Yehova akhazikitse mau ace. Comweco mkaziyo anakhala nayamwitsa mwana wace, kufikira anamletsa kuyamwa.
24 Ndipo atamletsa kuyamwa anakwera naye, pamodzi ndi ng'ombe ya zaka zitatu, ndi efa wa ufa, ndi thumba la vinyo, nafika naye ku nyumba ya Yehova ku Silo; koma mwanayo anali wamng'ono.