1 Ndipo caka cakhumi mphambu zisanu ndi zitatu ca Yerobiamu, Abiya analowa ufumu wa Yuda.
2 Anakhala mfumu m'Yerusalemu zaka zitatu; ndi dzina la mace ndiye Mikaya mwana wamkazi wa Uriyeli wa ku Gibeya. Ndipo panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yerobiamu.
3 Ndipo Abiya anayambana nkhondo ali ndi khamu la ngwazi za nkhondo, amuna osankhika zikwi mazana anai; Yerobiamu atandandalitsa nkhondo yace ilimbane naye ndi amuna osankhika zikwi mazana asanu ndi atatu, ndiwo ngwazi zamphamvu.
4 Ndipo Abiya anaimirira pa phiri la Zemaraimu, ndilo ku mapiri a Efraimu, nati, Mundimvere Yerobiamu ndi Aisrayeli onse;
5 simudziwa kodi kuti Yehova Mulungu wa Israyeli anapereka ciperekere ufumu wa Israyeli kwa Davide, kwa iye ndi ana ace, ndi pangano la mcere?