4 Ndipo Abiya anaimirira pa phiri la Zemaraimu, ndilo ku mapiri a Efraimu, nati, Mundimvere Yerobiamu ndi Aisrayeli onse;
5 simudziwa kodi kuti Yehova Mulungu wa Israyeli anapereka ciperekere ufumu wa Israyeli kwa Davide, kwa iye ndi ana ace, ndi pangano la mcere?
6 Koma Yerobiamu mwana wa Nebati mnyamata wa Solomo mwana wa Davide anauka, napandukana ndi mbuye wace.
7 Ndipo anamsonkhanira amuna acabe, anthu opanda pace, ndiwo anadzilimbikitsa kutsutsana naye Rehabiamu mwana wa Solomo, muja Rehabiamu anali mnyamata ndi woolowa mtima, wosakhoza kuwalaka.
8 Ndipo tsopano, mukuti mudzilimbikitse kutsutsana nao ufumu wa Yehova m'dzanja la ana a Davide; ndinu aunyinji ambiri, ndi pamodzi nanu ana a ng'ombe agolidi adawapanga Yerobiamu akhale milungu yanu.
9 Simunapitikitsa kodi ansembe a Yehova, ana a Aroni, ndi Alevi, ndi kudziikira ansembe monga amacita anthu a m'maiko ena? kuti ali yense wakudza kudzipatulira ndi mwana wa ng'ombe, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri, yemweyo ndiye wansembe wa iyo yosati milungu.
10 Koma ife, Yehova ndiye Mulungu wathu, sitinamsiya Iye; ndi ansembe tiri nao akutumikira Yehova ana a Aroni, ndi. Alevi, m'nchito mwao,