7 Ndipo Zikiri munthu wamphamvu wa Efraimu anapha Maseya mwana wa mfumu, ndi Azrikamu woyang'anira nyumba, ndi Elikana wotsatana ndi mfumu.
8 Ndipo ana a Israyeli anatenga ndende ena a abale ao zikwi mazana awiri, akazi, ana amuna ndi akazi, nalandanso kwa iwo zofunkha zambiri, nabwera nazo zofunkhazo ku Samariya,
9 Koma panali mneneri wa Yehova pomwepo, dzina lace Odedi; naturuka iye kukomana nayo nkhondo ikudzayo ku Samariya, nanena nao, Taonani, popeza Yehova Mulungu wa makolo anu anakwiya ndi Yuda, anawapereka m'dzanja lanu, nimunawapha ndi kupsa mtima kofikira kumwamba.
10 Ndipo tsopano mukuti mugonjetse ana a Yuda ndi Yerusalemu akhale akapolo ndi adzakazi anu; palibe nanunso kodi mirandu yoparamula kwa Yehova Mulungu wanu?
11 Mundimvere tsono, bwezani andende amene munawatenga ndende a abale anu; pakuti mkwiyo waukali wa Yehova uli pa inu.
12 Pamenepo akuru ena a ana a Efraimu, Azariya mwana wa Yohanana, Berekiya mwana wa Mesilemoti, ndi Yehizikiya mwana wa Salumu, ndi Amasa mwana wa Hadilai, anaukira aja ofuma kunkhondo,
13 nanena nao, Musalowa nao andende kuno; pakuti inu mukuti mutiparamulitse kwa Yehova, kuonjezera pa macimo athu ndi zoparamula zathu; pakuti taparamula kwakukuru, ndipo pali mkwiyo waukali pa Israyeli.