11 Pamenepo anaphera Paskha; ndi ansembe anawaza mwazi adaulandira m'manja mwa Alevi amene anasenda nsembezo.
12 Ndipo anacotsapo nsembe zopsereza, kuti azipereke kwa ana a anthu monga mwa magawidwe a nyumba za makolo; azipereke kwa Yehova monga mulembedwa m'buku la Mose. Natero momwemo ndi ng'ombezo.
13 Ndipo anaoca Paskha pamoto, monga mwa ciweruzo; koma zopatulikazo anaziphika m'miphika, ndi m'mitsuko, ndi m'ziwaya; nazipereka msanga kwa ana onse a anthu.
14 Ndi pambuyo pace anadzikonzera okha ndi ansembe; popeza ansembe, ana a Aroni, analikupereka nsembe zopsereza ndi mafuta mpaka usiku; cifukwa cace Alevi anadzikonzera okha ndi ansembe ana a Aroni.
15 Ndi oyimbira, ana a Asafu, anali pokhala pao, monga adalamulira Davide, ndi Asafu, ndi Hemani, ndi Yedutuni mlauli wa mfumu; ndi olindirira anali pa zipata zonse, analibe kuleka utumiki wao; pakuti abale ao Alevi anawakonzera
16 Momwemo kutumikira konse kwa Yehova kunakonzeka tsiku lomwelo, kucita Paskha, ndi kupereka nsembe zopsereza pa guwa la nsembe la Yehova, monga analamulira mfumu Yosiya.
17 Ndipo ana a Israyeli okhalako anacita Paskha nthawi yomweyo, ndi madyerero a mkate wopanda cotupitsa masiku asanu ndi awiri.