19 Ndipo anamwino ananena ndi Farao, Popeza akazi a Ahebri safanana ndi akazi a Aigupto; pakuti ali ndi mphamvu, naona ana asanalike anamwino.
20 Potero Mulungu anawacitira zabwino anamwino; ndipo anthuwo anacuruka, nakhala nazo mphamvu zazikuru.
21 Ndipo kunatero kuti, popeza anamwino anaopa Mulungu, iye anawamangitsira mabanja.
22 Ndipo Farao analamulira anthu ace onse, ndi kuti, Ana amuna onse akabadwa aponyeni m'nyanja, koma ana akazi onse alekeni amovo.