Eksodo 25 BL92

Zopereka zaufulu zakumanga Malo Opatulika

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

2 Lankhula ndi ana a Israyeli, kuti anditengere copereka; ulandire copereka canga kwa munthu ali yense mtima wace umfunitsa mwini.

3 Ndipo coperekaco ucilandire kwa iwo ndi ici: golidi, ndi, siliva, ndi mkuwa,

4 ndi lamadzi, ndi: lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi ubweya wa mbuzi;

5 ndi zikopa za nkhosa zamphongo zonika zofiira, ndi zikopa za akatumbu, ndi mtengo wasitimu;

6 mafuta akuunikira, zonunkhira za mafuta odzoza, ndi za cofukiza ca pfungo lokoma;

7 miyala yaberulo, ndi miyala yoika paefodi, ndi pacapacifuwa.

8 Ndipo andimangire malo opatulika; kuti ndikhale pakati pao,

9 Monga mwa zonse Ine ndirikuonetsa iwe, cifaniziro ca kacisi, ndi cifaniziro ca zipangizo zace zonse, momwemo ucimange.

Za likasa, cotetezerapo, ndi akerubi

10 Ndipo azipanga likasa la mtengo wasitimu: utali wace mikono iwiri ndi hafu, kupingasa kwace mkono ndi hafu, msinkhu wace mkono ndi hafu.

11 Ndipo ulikute ndi golidi woona, ulikute m'kati ndi kubwalo, nulipangire mkombero wagolidi pozungulira pace.

12 Ndipo uliyengere mphete zinai zagolidi, ndi kuziika ku miyendo yace inai; mphete ziwiri pa mbali yace yina, ndi mphete ziwiri pa yina.

13 Ndipo uzipanga mphiko za mtengo wasitimu, ndi kuzikuta ndi golidi.

14 Nupise mphiko m'mphetezo pa mbali zace za likasa, zakunyamulira nazo likasalo.

15 Mphiko zikhale m'zimphete za likasa; asazisolole.

16 Ndipo uziika m'likasamo mboni imene ndidzakupatsa.

17 Ndipo uzipanga cotetezerapo ca golidi woona; utali wace mikono iwiri ndi hafu, ndi kupingasa kwace mkono ndi hafu.

18 Uzipanganso akerubi awiri agolidi; uwasule mapangidwe ace, pa mathungo ace awiri a cotetezerapo.

19 Nupange kerubi mmodzi ku thungo lino, ndi kerubi wina ku thungo lina; upange akerubi ocokera kucotetezerapo, pa mathungo ace awiri.

20 Ndipo akerubi afunyululire mapiko ao m'mwamba, ndi kuphimba cotetezerapo ndi mapiko ao, ndi nkhope zao zipenyane; nkhope za akerubi ziphenye kucotetezerapo,

21 Ndipo uziika cotetezerapo pamwamba pa likasa, ndi kuikamo mboni ndidzakupatsayo m'likasamo.

22 Ndipo pomwepo ndidzakomana ndi iwe, ow kulankhula ndi iwe, ndiri pamwamba pa cotetezerapo, pakati pa akerubi awiriwo okhala pa likasa la mboni, zonse zimene ndidzakuuza za ana a Israyeli.

Za gome la mkate woonekera

23 Ndipo uzipanga gome la mtengo wasitimu; utali wace mikono iwiri, ndi kupingasa kwace mkono umodzi, ow msinkhu wace mkono ndi hafu.

24 Ndipo ulikute ndi golidi woona ndi kulipangira mkombero wagolidi pozungulira pace.

25 Nulipangire mitanda pozungulirapo yoyesa cikhato m'kupingasa kwace, ndi pamitanda pace pozungulira upangirepo mkombero wagolidi.

26 Nulipangire mphete zinai zagolidi, ndi kuika mphetezo pa ngondya zinai zokhala pa miyendo yace inai.

27 Mphetezo zikhale pafupi pa mitanda, zikhale zopisamo mphiko za kunyamulira nazo gome.

28 Ndipo uzipanga mphiko za mtengo wasitimu, ndi kuzikuta ndi golidi, kuti anyamulire nazo gome.

29 Ndipo uzipanga mbale zace, ndi zipande zace, ndi mitsuko yace, ndi zikho zace zakuthira nazo; uzipanga za golidi woona.

30 Ndipo uziikamkate woonekera pa gomelo pamaso panga nthawi zonse.

Za coikapo nyali

31 Ndipo uzipanga coikapo nyali ca golidi woona; coikapoco cisulidwe mapangidwe ace, tsinde lace ow thupi lace; zikho zace, mitu yace, ndi maluwa ace zikhale zocokera m'mwemo;

32 ndipo m'mbali zace muturuke mphanda zisanu ndi imodzi; mphanda zitatu za coikapo nyalico zituruke m'mbali yace yina, ndi mphanda zitatu za coikapo nyalico zituruke m'mbali inzace.

33 Ku mphanda yina kukhale zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi luwa; ndi ku mphanda inzace zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi luwa; zitere mphanda zisanu ndi imodzi zoturuka m'coikapo nyalico.

34 Ndipo pa coikapo nyali comwe pakhale zikho zinai zopangika ngati katungurume, mitu yace ndi maluwa ace;

35 pakhale mutu pansi pa mphaada ziwiri zoturuka m'mwemo, ndi mutu pansi pa mphanda ziwiri zoturuka m'mwemo, ndi mutu pansi pa mphanda ziwiri zoturuka m'mwemo; itere ku mphanda zisanu ndi imodzi zoturuka m'coikapo nyalico.

36 Mitu yao ndi mphanda zao zikhale zoturuka m'mwemo; conseci cikhale cosulika cimodzi ca golidi woona.

37 Ndipo uzipanga nyali zace, zisanu ndi ziwiri; ndipo ayatse nyali zace, ziwale pandunji pace.

38 Ndipo mbano zace, ndi zoolera zace, zikhale za golidi woona.

39 Acipange ici ndi zipangizo izi zonse za talente wa golidi woona.

40 Ndipo uyang'anire uzipanga monga mwacifaniziro cao, cimene anakuonetsa m'phirimo.