Eksodo 34 BL92

Magome atsopano a Malamulowo

1 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Dzisemere magome awiri amiyala onga oyamba aja; ndipo ndidzalembera pa magomewo mau omwewo anali pa magome oyambawo, amene unawaswa.

2 Nukonzekeretu m'mawa, nukwere m'mawa m'phiri la Sinai, nuimepo pamaso panga pamwamba pa phiri.

3 Palibe munthu akwere ndi iwe, asaonekenso munthu ali yense m'phiri monse; ndi zoweta zazing'ono kapena zoweta zazikuru zisadye kuphiri kuno.

4 Ndipo anasema magome awiri a miyala, onga oyamba aja; ndipo Mose anauka mamawa nakwera m'phiri la Sinai, monga Yehova adamuuza, nagwira m'dzanja mwace magome awiri amiyala.

5 Ndipo Yehova anatsika mumtambo, naimapo pamodzi ndi iye, napfuula dzina la Yehova.

6 Ndipo Yehova anapita pamaso pace, napfuula, Yehova, Yehova, Mulungu wacifundo ndi wacisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wocuruka, ndi wacoonadi;

7 wakusungira anthu osawerengeka cifundo, wakukhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kucimwa; koma wosamasula woparamula; wakulangira ana ndi zidzukulu cifukwa ca mphulupulu ya atate ao, kufikira mbadwo wacitatu ndi wacinai.

8 Ndipo Mose anafulumira, naweramira pansi, nalambira.

9 Ndipo anati, Ngati ndapeza ufulu tsopane pamaso panu, Ambuye, ayendetu Ambuye pakati pa ife; pakuti awa ndi anthu opulupudza; ndipo mutikhululukire mphulupulu ndi ucimo wathu, ndipo mutilandire tikhale colowa canu.

10 Ndipo iye anati, Taona, Ine ndicita pangano; ndidzacita zozizwa pamaso pa anthu ako onse, sizinacitika zotere ku dziko lonse lapansi, kapena ku mtundu uti wonse wa anthu; ndipo anthu onse amene uli pakati pao adzaona nchito ya Yehova, pakuti cinthu ndikucitiraci ncoopsa.

11 Dzisungire cimene Ine ndikuuza lero lino: taona, ndiingitsa pamaso pako Aamori ndi Akanani, ndi Ahiti ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi.

12 Dzicenjere ungacite pangano ndi anthu a ku dziko limene umukako, lingakhale msampha pakati panu;

13 koma mupasule maguwa a nsembe ao, ndi kuphwanya zoimiritsa zao, ndi kulikha zifanizo zao;

14 pakuti musalambira mulungu wina; popeza Yehova dzina lace ndiye Wansanje, ali Mulungu wansanje;

15 ungacite pangano ndi iwo okhala m'dzikomo; ndipo angacite cigololo pakutsata milungu yao, nangaphere nsembe milungu yao, ndipo angakuitane wina, nukadye naye nsembe zace;

16 ndipo ungatengereko ana ako amuna ana ao akazi; nangacite cigololo ana ao akazi potsata milungu yao, ndi kucititsa ana anu amuna cigololo potsata milungu yao.

17 Usadzipangire milungu yoyenga.

18 Uzisunga madyerero a mkate wopanda cotupitsa. Uzidya mkate wopanda cotupitsa masiku asanu ndi awiri, monga ndakuuza pa nthawi yonenedwa, m'mwezi wa Abibu; pakuti mwezi wa Abibu unaturuka m'Aigupto.

19 Onse oyambira kubadwa ndi anga; ndi zoweta zanu zonse zazimuna, zoyamba za ng'ombe ndi za nkhosa.

20 Koma woyamba wa buru uzimuombola ndi mwana wa nkhosa; ukapanda kumuombola, uzimthyola khosi. Ana anu amuna oyamba onse uziwaombola. Ndipo asamaoneka pamaso panga opanda kanthu.

21 Masiku asanu ndi limodzi uzigwira nchito, koma lacisanu ndi ciwiri uzipumula; nyengo yakulima ndi nyengo yamasika uzipumula.

22 Ndipo uzicita madyerero a masabata, ndiwo madyerero a zipatso zoyamba za masika a tirigu, ndi madyerero a kututa pakutha pa caka.

23 Amuna ako onse azioneka pamaso pa Yehova Mulungu, Mulungu wa Israyeli, katatu caka cimodzi.

24 Pakuti ndidzaingitsa mitundu ya anthu pamaso pako, ndi kukulitsa malire ako; ndipo palibe munthu adzakhumba dziko lako, pakukwera iwe kudzaoneka pamaso pa Yehova Mulungu wako katatu caka cimodzi.

25 Usapereke mwazi wa nsembe yanga yophera pamodzi ndi mkate wacotupitsa; ndi nsembe yophera ya madyerero a Paskha asaisiye kufikira m'mawa.

26 Uzibwera nazo zipatso zoyambayamba za nthaka yako ku nyumba ya Yehova Mulungu wako. Usaphika mwana wa mbuzi mu mkaka wa mace.

27 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ulembere mau awa; pakuti monga mwa mau awa ndapangana ndi iwe ndi Israyeli.

28 Ndipo anakhala pomwepo ndi Yehova masiku makumi anai, usana ndi usiku; sanadya mkate kapena kumwa madzi. Ndipo analembera pa magomewo mau a panganolo, mau khumiwo.

Nkhope ya Mose inyezimira

29 Ndipo kunali pakutsika Mose pa phiri la Sinai, ndi magome awiri a mboni m'dzanja lace la Mose, pakutsika iye m'phirimo, Mose sanadziwa kuti khungu la nkhope yace linanyezimira popeza iye adalankhula naye.

30 Ndipo pamene Aroni ndi ana onse a Israyeli anaona Mose, taonani, khungu la nkhope yace linanyezimira; ndipo anaopa kumyandikiza.

31 Koma Mose anawaitana; ndipo Aroni ndi akazembe onse a khamu la anthu anabwera kwa iye; ndipo Mose analankhula nao.

32 Ndipo atatero, ana onse a Israyeli anayandikiza; ndipo iye anawauza zonse Yehova adalankhula naye m'phiri la Sinai.

33 Ndipo Mose atatha kulankhula nao, anaika cophimba pankhope pace.

34 Koma pakulowa Mose pamaso pa Yehova kunena ndi iye, ariacotsa cophimbaco, kufikira akaturuka; ndipo ataturuka analankhula ndi ana a Israyeli cimene adamuuza.

35 Ndipo ana a Israyeli anaona nkhope ya Mose, kuti khungu la nkhope ya Mose linanyezimira; ndipo Mose anaikanso cophimba pankhope pace, kufikira akalowa kulankhula ndi iye.