1 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka, kwera kucokera kuno, iwe ndi anthu amene unawakweza kucokera m'dziko la Aigupto, kumka ku dzikolo ndinalumbirira nalo Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo, ndi kuti, Ndidzapatsa mbeu zako ilo;
2 ndipo ndidzatuma mthenga akutsogolere; ndipo ndidzapitikitsa Akanani, ndi Aamori, ndi Ahiti, ndi Aperizi, Ahivi, ndi Ayebusi;
3 kudziko koyenda mkaka ndi uci ngati madzi; pakuti sindidzakwera pakati pa inu; popeza inu ndinu anthu opulupudza; ndingathe inu panjira.
4 Ndipo pamene anthu anamva mau awa oipa anacita cisoni; ndipo panalibe mmodzi anabvala zokometsera zace.
5 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi ana a Israyeli, Inu ndinu anthu opulupudza; ndikakwera kulowa pakati pa inu kamphindi kamadzi, ndidzakuthani; koma tsopano, bvulani zokometsera zanu, kuti ndidziwe comwe ndikucitireni.
6 Ndipo ana a Israyeli anazicotsera zokometsera zao kuyambira pa phiri la Horebe.
7 Ndipo Mose akatenga cihemaco nacimanga kunja kwa cigono, kutari kwa cigono; nacicha, Cihema cokomanako. Ndipo kunakhala kuti yense wakufuna Yehova anaturuka kumka ku cihema cokomanako kunja kwa cigono.
8 Ndipo kunali, pakuturuka Mose kumka ku cihemaco kuti anthu onse anaimirira, nakhala ciriri, munthu yense pakhomo pa hema wace, nacita cidwi pa Mose, kufikira atalowa m'cihemaco.
9 Ndipo kunali, pakulowa Mose m'cihemaco, mtambo njo udafutsika, nuima pakhomo pa cihemaco; ndipo Yehova analankhula ndi Mose.
10 Ndipo anthu onse anaona mtambo njo ulikuima pakhomo pa cihema; ndi anthu onse anaimirira, nalambira, yense pakhomo pa hema wace.
11 Ndipo Yehova ananena ndi Mose kopenyana maso, monga munthu alankhula ndi bwenzi lace. Ndipo anabwerera kumka kucigono; koma mtumiki wace Yoswa, mwana wa Nuni, ndiye mnyamata msinkhu wace, sanacoka m'cihemamo.
12 Ndipo Mose anati kwa Yehova, Taonani, Inu munena ndi ine, Kwera nao anthu awa; koma simunandidziwitsa amene mudzamtuma amuke nane. Koma munati, Ndikudziwa dzina lako, wapezanso ufulu pamaso panga,
13 Ndipo tsopano, ngati ndapeza ufulu pamaso panu, mundidziwitsetu njira zanu, kuti ndikudziweni, ndi kuti ndipeze ufulu pamaso panu; ndipo penyani kuti mtundu uwu ndi anthu anu.
14 Ndipo anati, Nkhope yanga idzamuka nawe, ndipo ndidzakupumuza.
15 Ndipo ananena ndi Iye, Ikapanda kumuka nane nkhope yanu, musatikweze kucokera kuno.
16 Pakuti cidziwfka ndi ciani tsopano kuti ndapeza ufulu pamaso panu, ine ndi anthu anu? Si pakumuka nafe Inu, kuti ine ndi anthu anu tisiyane ndi anthu onse akukhala pa nkhope ya dziko lapansi?
17 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ici comwe wanenaci ndidzacita; pakuti wapeza ufulu pamaso panga, ndipo ndikudziwa dzina lako.
18 Ndipo anati, Ndionetsenitu ulemerero wanu.
19 Ndipo iye anati, Ndidzapititsa ukoma wanga wonse pamaso pako, ndipo ndidzachula dzina la Yehova pamaso pako; ndipo ndidzacitira ufulu amene ndidzamcitira ufulu; ndi kucitira cifundo amene ndidzamcitira cifundo.
20 Ananenanso, Sungathe kuona nkhope yanga; pakuti palibe munthu adzandiona Ine ndi kukhala ndi moyo.
21 Ndipo Yehova anati, Taona pali Inepo pali malo, ndipo uime pathanthwe;
22 ndipo kudzakhala, pakupitira olemerero wanga, ndidzakuika mu mpata wa thanthwe, ndi kukuphimba ndi dzanja langa, mpaka nditapitira;
23 ndipo pamene ndicotsa dzanja langa udzaona m'mbuyo mwanga; koma nkhope yanga siidzaoneka.