1 Ndipo Bezaleli anapanga likasa la mtengo wasitimu; utali wace mikono iwiri ndi hafu, ndi kupingasa kwace mkono ndi hafu, ndi msinkhu wace mkono ndi hafu;
2 ndipo analikuta ndi golidi woona m'kati ndi kunja, nalipangira mkombero wagolidi pozungulira pace.
3 Ndipo analiyengera mphete zinai zagolidi pa miyendo yace inai; mphete ziwiri pa mbali yace imodzi, ndi mphete: ziwiri pa mbali yace yina.
4 Ndipo anapanga mphiko za mtengo wasitimu, nazikuta ndi golidi.
5 Ndipo anapisa mphiko m'mphetezo pa mbali zace za likasalo, kuti anyamulire nazo likasa.
6 Ndipo anapanga cotetezerapo ca golidi woona; utali wace mikono iwiri ndi hafu, ndi kupingasa kwace mkono ndi hafu.
7 Anapanganso akerubi awiri agolidi; anacita kuwasula mapangidwe ace, pa mathungo ace swiri a coteteze rapo;
8 kerubi mmodzi pa mbali yace imodzi, ndi kerubi wilia pa mbali yace yina; anapanga akerubi ocokera m'cotetezerapo, pa mathungo ace awiri.
9 Ndipo akerubi anafunyulira mapiko ao m'mwamba, ndi kuphimba cotetezerapo ndi mao piko ao, ndi nkhope zao zopeoyana; zinapenya kucotetezerapo nkhope zao.
10 Ndipo anapanga gome la mtengo wasitimu; utali wace mikono iwiri, ndi kupingasa kwace mkono limodzi, ndi msinkhu wace mkono ndi hafu;
11 ndipo analikuta ndi golidi woona, nalipangira mkombero wagolidi pozungulira pace.
12 Analipangiranso mitanda pozungulirapo, yoyesa cikhato m'kupingasa kwace, ndi pamitanda pace pozungulira anapangirapo mkombero wagolidi.
13 Ndipo analiyengera mphete zinai zagolidi, naika mphetezo pa ngondya zace zinai zokhala pa miyendo yace inai.
14 Mphetezo zinali pafupi pa mitanda, zikhale zopisamo mphiko kunyamulira nazo gomelo.
15 Ndipo anapanga mphiko za mtengo wasitimu, nazikuta ndigolidi, kunyamulira nazo gomelo.
16 Anapanganso zipangizo za gomelo, mbale zace, ndi zipande zace, ndi mitsuko yace, ndi zikho zace zakuthira nazo, za golidi woona.
17 Ndipo anapanga coikapo nyali ca golidi woona; mapangidwe ace a coikapo nyalico anacita cosula, tsinde lace ndi thupi lace, zikho zace, mitu yace, ndi maluwa ace zinakhala zocokera m'mwemo;
18 ndi m'mbali zace munaturuka mphanda zisanu ndi imodzi; mphanda zitatu za coikapo nyali zoturuka m'mbali yace imodzi, ndi mphanda zitatu za coikapo nyali zoturuka m'mbali yace yina;
19 pa mphanda imodzi panali zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi luwa; ndi pa mphanda yina zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi luwa; zinatero mphanda zisanu ndi imodzi zoturuka m'coikapo nyali.
20 Ndipo pa coikapo nyali comwe panali zikho zinai zopangika ngati katungurume, mitu yace ndi maluwa ace;
21 ndipo panali mutu pansi pa mphanda ziwiri, zoturuka m'mwemo, ndi mutu pansi pa mphanda ziwiri, zoturuka m'mweno, ndi mutu pansi pa mphanda ziwiri, zoturuka m'mwemo, inatero pa mphanda zisanu ndi imodzi zocokera m'mwemo.
22 Mitu yao ndi mphanda zao zinaturuka m'mwemo; conseci cinali cosulika pamodzi ca golidi woona.
23 Ndipo anapanga nyali zace zisanu ndi ziwiri ndi mbano zace, ndi zoolera zace, za golidi woona.
24 Anacipanga ici ndi zipangizo zace zonse za talente wa golidi woona.
25 Ndipo anapanga guwa la nsembe lofukizapo la mtengo wasitimu; utali wace mkono, ndi kupingasa kwace mkono, lampwamphwa; ndimsinkhu wace mikono iwiri; nyanga zace zinaturuka m'mwemo.
26 Ndipo analikuta ndi golidi woona, pamwamba pace, ndi mbali zace pozungulira, ndi nyanga zace; ndipo analipangira mkombero wagolidi pozungulira pace.
27 Ndipo analipangira mphete ziwiri zagolidi pansi pa mkombero wace, pa ngondya zace ziwiri, pa mbali zace ziwiri, zikhale zopisamo mphiko kulinyamulira nazo.
28 Ndipo anazipanga mphiko za mtengo wasitimu, nazikuta ndi golidi.
29 Anapanganso mafuta opatulika akudzoza nao, ndi cofukiza coona ca pfungo lokoma, mwa macitidwe a wosanganiza.