Eksodo 35 BL92

Zopereka zofunika za pa cihemaco

1 Ndipo Mose anasonkhanitsa khamu lonse la ana a Israyeli, nanena nao, Siwa mau amene Yehova anauza, kuti muwacite.

2 Masiku asanu ndi limodzi azigwira nchito; koma tsiku lacisanu ndi ciwiri muliyese lopatulika, Sabata lakupuma la Yehova: ali yense agwira nchito pamenepo, aphedwe,

3 Musamasonkha mota m'nyumba zanu ziri zonse tsiku la Sabata.

4 Ndipo Mose ananena ndi khamu lonse la ana a Israyeli, ndi kuti, Ici ndi cimene Yehova anauza ndi kuti,

5 Mumtengere Yehova copereka ca mwa zanu; ali yense wa mtima womfunitsa mwini abwere naco, ndico copereka ca Yehova;

6 golidi, ndi siliva, ndi mkuwa; ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi ubweya wa mbuzi;

7 ndi zikopa za nkhosa zamphongo zonika zofiira, ndi zikopa za akatumbu, ndi mtengo wasitimu;

8 ndi mafuta akuunikira, ndi zonunkhira za mafuta odzoza, ndi cofukiza ca pfungo lokoma;

9 ndi miyala yasohamu, ndi miyala yoika ya efodi, ndi ya capacifuwa.

10 Ndipo abwere yense wa mtima waluso mwa inu, napange zonse zimene Yehova anauza;

11 kacisi, hema wace, ndi cophimba cace, zokowera zace, ndi matabwa ace, mitanda yace, mizati, nsanamira, ndi nsici zace, ndi makamwa ao;

12 likasa, ndi mphiko zace, cotetezerapo, ndi nsaru yocinga yotseka;

13 gome, ndi mphiko zace, ndi zipangizo zace zonse, ndi mkate woonekera;

14 ndi coikapo nyali ca kuunika, ndi zipangizo zace, ndi nyali zace, ndi mafuta a kuunika;

15 ndi guwa la nsembe lofukizapo, ndi mphiko zace, ndi mafuta odzoza, ndi cofukiza ca pfungo lokoma, ndi nsaru yotsekera pakhomo, pa khomo la kacisi;

16 guwa la nsembe yopereza, ndi made amkuwa, mphiko zace, ndi zipangizo zace zonse, mkhate ndi tsinde lace;

17 nsaru zocingira za kubwalo, nsici zace, ndi makamwa ace, ndi nsaru yotsekera ku cipata ca pabwalo;

18 ziciri za cihema, ndi ziciri za kubwalo, ndi zingwe zao;

19 zobvala za kutumikira nazo m'maopatulika, zobvala zopatulika za. Aroni wansembe, ndi zobvala za ana ace, zakugwira nazo nchito ya nsembe.

Anthu abwera ndi zopereka mwaufulu

20 Ndipo khamu lonse la ana a Israyeli linacoka pamaso pa Mose.

21 Ndipo anadza, ali yense wofulumidwa mtima, ndi yense mzimu wace wamfunitsa, nabwera naco copereka ca Yehova, ca ku nchito ya cihema cokomanako, ndi ku utumiki wace wonse, ndi ku zobvala zopatulika.

22 Ndipo anadza amuna ndi akazi, onse akufuna mtima eni ace, nabwera nazo mphete za mphuno, mphete za m'makutu, ndi mphete zosindikizira, ndi zidzingwiri, zonsezi zokometsera zagolidi; inde yense wakupereka kwa Yehova copereka cagolidi.

23 Ndipo ali yense kwao kunapezeka lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi ubweya wa mbuzi, ndi zikopa za nkhosa zamphongo zonika zofiira, ndi zikopa za akatumbu, anabwera nazo.

24 Yense wakupereka copereka ca siliva ndi mkuwa, anabwera naco copereka ca Yehova; ndi yense amene kwao kunapezeka mtengo wasitimu wa ku macitidwe onse a nchitoyi, anabwera nao.

25 Ndi akazi onse a mtima waluso anapota ndi manja ao, nabwera nalo thonje lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.

26 Ndi akazi onse ofulumidwa mtima ndi luso anapota ubweyawo wa mbuzi.

27 Ndi akuru anabwera nayo miyala yasohamu, ndi miyala yoti aiike kuefodi, ndi kucapacifuwa;

28 ndi zonunkhira, ndi mafuta akuunikira, ndi mafuta odzoza, ndi cofukiza za pfungo lokoma.

29 Amuna ndi akazi onse a ana a Israyeli amene mitima yao inawafunitsa eni kubwera nazo za ku nchito yonse imene Yehova anauza Ipangike ndi dzanja la Mose, anabwera naco copereka cofuna mwini, kucipereka kwa Yehova.

30 Ndipo Mose anati kwa ana a Israyeli, Taonani, Yehova anaitana, ndi kumchula dzina lace, Bezaleli, mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa pfuko la Yuda;

31 ndipo anamdzaza ndi mzimu wa Mulungu, ndi luso, ndi nzeru, ndi cidziwitso, za m'nchito ziri zonse;

32 kulingirira nchito zaluso, kucita ndi golidi, ndi siliva, ndi mkuwa;

33 ndi kuzokota miyala voikika, ndi kuzokota mitengo, kucita m'nchito ziri zonse zaluso.

34 Ndipo anaika m'mtima mwace kuti alangize ena, iye ndi Aholiabu mwana wa Ahisama, wa pfuko la Dani.

35 Amenewo anawadzaza ndi luso lamtima, lakucita nchito ziri zonse, ya kuzokota miyala, ndi ya mmisiri waluso, ndi ya wopikula ndi lamadzi ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi ya muomba, ya iwo akucita nchito iri yonse, ndi ya iwo olingirira nchito yaluso.