Eksodo 39 BL92

Maombedwe a zobvala za ansembe

1 Ndipo anaomba zobvala zakutumikira nazo ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, atumikire nazo m'malo opatulika, naomba zobvala zopatulika za Aroni; monga Yehova adamuuza Mose.

2 Ndipo anaomba efodi wa golidi, lamadzi, lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.

3 Ndipo anasula golidi waphanthiphanthi, nalemba nsambo, kuti amuombe pamodzi ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, nchito ya mmisiri.

4 Anapangira efodi zapamapewa zolumikizana; pa nsonga ziwirizo anamlumikiza.

5 Ndi mpango wa efodi wokhala pamenepo, wakummanga nao unali woombera kumodzi wa ciombedwe comweci; wa golidi, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa; monga Yehova adauza Mose.

6 Ndipo anakonza miyala yasohamu, yogwirika m'zoikamo zagolidi, yoloca ngati malocedwe a cosindikizira, ndi maina a ana a lsrayeli.

7 Ndipo anaiika pa zapamapewa za efodi, ikhale miyala ya cikumbutso kwa ana a Israyeli; monga Yehova adamuuza Mose.

8 Ndipo anaomba capacifuwa, nchito ya mmisiri, monga maombedwe ace a efodi; ca golidi, lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.

9 Cinakhala camowamphwa; anaciomba capacifuwa copindika; utali wace cikhato cimodzi, ndi kupingasa kwace cikhato cimodzi, cinakhala copindika.

10 Ndipo anaika pomwepo mizere inai ya miyala; mzere wa odemu, pitida, ndi bareketi, ndiyo ya mzere woyamba.

11 Ndi mzere waciwiri wa nofeki, safiri, ndi yahalomu.

12 Ndi mzere wacitatu wa lesemu, sibu, ndi akalama.

13 Ndi mzere wacinai wa tarisisi, sohamu, ndi yasefe; inakhala yogwirika ndi golidi maikidwe ace.

14 Ndipo miyalayi inakhala monga mwa maina a ana a Israyeli, khumi ndi awiri, monga mwa maina ao; ngati malocedwe a cosindikizira, yonse monga mwa maina ace, kwa mafuko khumi ndi awiriwo.

15 Ndipo anapangira pacapacifuwa maunyolo ngati zingwe, nchito yopota ya golidi woona.

16 Anapanganso zoikamo ziwiri zagolidi, ndi mphete ziwiri zagolidi; naika mphete ziwirizo pa nsonga ziwiri za capacifuwa.

17 Ndipo anamanga maunyolo awiri opota agolidi pa mphete ziwiri pa nsonga za capacifuwa.

18 Ndi nsonga zace ziwiri zina za maunyolo awiri opotawo anazimanga pa zoikamo ziwiri, nazimanga pa zapamapewa za efodi, m'tsogolo mwace.

19 Ndipo anapanga mphete ziwiri zagolidi, naziika pa nsonga ziwiri za capacifuwa, m'mphepete mwace m'katimo, pa mbali ya kuefodi.

20 Ndipo anapanga mphete ziwiri zagolidi, naziika pa zapamapewa ziwiri za efodi pansi pace, pa mbali yace ya kutsogolo, pafupi pa msoko wace, pamwamba pa mpango wa efodi.

21 Ndipo anamanga capacifuwa pa mphete zace ndi mphete za efodi ndi mkuzi wamadzi, kuti cikhale pa mpango wa efodi, ndi kuti capacifuwa cisamasuke paefodi; monga Yehova anamuuza Mose.

22 Ndipo anaomba mwinjiro wa efodi, nchito yoomba ya lamadzi lokha;

23 ndi pakati pace polowa mutu, ngati polowa pa maraya ocingirizira, ndipo anabinyira pozungulira polowa pace, pangang'ambike.

24 Napangira pa mkawo wa mwinjiro makangaza a lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.

25 Ndipo anapanga miriu ya golidi woona, napakiza miriu ndi makangaza, pa mkawo wa mwinjiro pozungulira, popakiza ndi makangaza.

26 Mliu ndi khangaza, mliu ndi khangaza pa mkawo wa mwinjiro pozungulira, kutumikira nazo; monga Yehova anamuuza Mose.

27 Ndipo anaomba maraya a bafuta, a nchito yoomba, a Aroni, ndi a ana ace amuna,

28 ndi nduwira va bafuta wa thonje losansitsa, ndi akapal okometsetsa a bafuta wa thonje losansitsa, ndi zobvala za kumiyendo za bafuta wa thonje losansitsa,

29 ndi mpango wabafuta wa thonje losansitsa, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, nchito ya wopikula; monga Yehova adamuuza Mose.

30 Ndipo anapanga phanthiphanthi wa korona wopatulika wa golidi woona, nalembapo lemba, ngati malocedwe a cosindikizira, KUPATULIKIRA YEHOVA.

31 Namangako mkuzi wamadzi, kuumanga nao pamwamba pa nduwira; monga Yehova adamuuza Mose.

32 Potero anatsiriza nchito yonseya kacisi wa cihema cokomanako; ndipo ana a Israyeli adacita monga mwa zonse Yehova adamuuza Mose, anacita momwemo.

Zopangidwa zonae zionetsedwa kwa Mose

33 Ndipo anabwera naye kacisi kwa Mose, cihemaco, ndi zipangizo zace zonse, zokowera zace, matabwa ace, mitanda yace, ndi mizati yace, nsanamira zace ndi nsici zace, ndi makamwa ace;

34 ndi cophimba ca zikopa za nkhosa zamphongo zonika zofiirira, ndi cophimba ca zikopa za akatumbu, ndi nsaru yocinga yotsekera;

35 likasa la mboni, ndi mphiko zace, ndi cotetezerapo;

36 gomelo, zipangizo zace zonse, ndi mkate woonekera;

37 coikapo nyali coona, nyali zace, ndizo nyali zimakonzekazi, ndi zipangizo zace zonse, ndi mafuta a kuunikira;

38 ndi guwa la nsembe lagolidi, ndi mafuta odzoza, ndi cofukiza ca pfungo lokoma, ndi nsaru yotsekera pa khomo la cihemaco;

39 guwa la nsembe lamkuwa, ndi made ace amkuwa, mphiko zace, ndi zipangizo zace zonse, mkhate ndi tsinde lace;

40 nsaru zocingira za pabwalo, osici zace, ndi makamwa ace, ndi nsaru yotsekera pa cipata ca pabwalo, zingwe zace, ndi ziciri zace, ndi zipangizo zonse za nchito ya kacisi, za ku cihema cokomanako;

41 zobvala zokoma za kutumikira nazo m'malo opatulika, ndi zobvala zopatulika za Aroni wansembe, ndi zobvala za ana ace, kucita nazo nchito ya usembe.

42 Monga mwa zonse Yehova adamuuza Mose, momwemo ana a Israyeli anacita nchito zonse.

43 Ndipo Mose anaona nchito zonse, ndipo, taonani, adaicita monga Yehova adamuuza, momwemo adacita. Ndipo Mose anawadalitsa.