Eksodo 19 BL92

Mulungu alamulira anthu za ku Sinai

1 Mwezi wacitatu ataturuka ana a Israyeli m'dziko la Aigupto, tsiku lomwelo, analowa m'cipululu ca Sinai.

2 Pakuti anacoka ku Refidimu, nalowa m'cipululu ca Sinai, namanga tsasa m'cipululumo; ndipo Israyeli anamanga tsasa pamenepo pandunji pa phirilo.

3 Ndipo Mose anakwera kwa Mulungu; ndipo Yehova ali m'phirimo anamuitana, ndi kuti, Uzitero kwa mbumba ya Yakobo, nunene kwa ana a Israyeli, kuti,

4 Inu munaona cimene ndinacitira Aaigupto; ndi kuti ndanyamula inu monga pa mapiko a mphungu, ndi kubwera nanu kwa Ine ndekha.

5 Ndipo tsopano, ngati mudzamvera mau anga ndithu, ndi kusunga cipangano canga, ndidzakuyesani cuma canga ca padera koposa mitundu yonse ya anthu; pakuti dziko lonse lapansi ndi langa;

6 ndipo ndidzakuyesani ufumu wanga wa ansembe, ndi mtundu wopatulika. Awa ndi mau amene ukalankhule ndi ana a lsrayeli.

7 Ndipo Mose anadza, naitana akuru a anthu, nawaikira pamaso pao mau awa onse amene Yehova adamuuza.

8 Ndipo anthu onse anabvomera pamodzi, nati, Zonse adazilankhula Yehova tidzazicita. Ndipo Mose anabwera nao mau a anthu kwa Yehova.

9 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ndikudza kwa iwe mu mtambo wakuda bii, kuti anthu amve pamene ndilankhula ndi iwe, ndi kuti akubvomereze nthawi zonse. Pakuti Mose adauza Yehova mau a anthuwo.

10 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka kwa anthuwo, nuwapatulitse lero ndi mawa, ndipo atsuke zobvala zao,

11 nakonzekeretu tsiku lacitatu; pakuti tsiku lacitatu Yehova adzatsika pa phiri la Sinai pamaso pa anthu onse.

12 Ndipo ukalembere anthu malire pozungulira, ndi kuti, Muzicenjera musakwere m'phiri, musakhudza cilekezero cace; wokhudza phirilo adzaphedwa ndithu;

13 dzanja liri lonse lisalikhudze, wakulikhudza azimponyatu miyala, kapena kumpyoza; ngakhale coweta ngakhale munthu, zisakhale ndi moyo. Pamene lipenga libanika liu lace azikwera m'phirimo.

14 Ndipo Mose anatsika m'phiri kumka kwa anthu, nawapatulitsa anthu; natsuka iwo zobvala zao.

15 Ndipo anati kwa anthu, Mukonzekeretu tsiku lacitatu nimusayandikiza mkazi.

16 Ndipo kunali tsiku lacitatu, m'mawa, panali mabingu ndi zimphezi, ndi mtambo wakuda bii paphiripo, ndi liu la lipenga lolimbatu; ndi anthu onse okhala kutsasa ananjenjemera.

17 Ndipo Mose anaturutsa anthu kutsasa, kuti akomane ndi Mulungu; ndipo anaima patsinde pa phiri.

18 Ndipo phiri la Sinai linafuka monsemo, popeza Yehova anatsikira m'moto pamenepo; ndi utsi wace unakwera ngati utsi wa m'ng'anjo, ndi phiri lonse linagwedezeka kwambiri,

19 Ndipo pamene liu la lipenga linamveka linakulira-kulira, Mose ananena, ndi Mulungu anamyankha ndi mau.

20 Ndipo Yehova anatsikira pa phiri la Sinai, pamutu pace pa phiri; ndipo Yehova anaitana Mose akwere pamutu pa phiri; ndi Mose anakwerapo.

21 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tsika, cenjeza anthu, kuti angapyolere kwa Yehova kudzaona, ndipo angagwe ambiri a iwowa.

22 Ansembenso, akuyandikiza kwa Yehova adzipatulitse, angawapasule Yehova.

23 Ndipo Mose anati kwa Yehova, Anthu sangathe kukwera m'phiri la Sinai; pakuti Inu mwaticenjeza, ndi kuti, Lemba malire m'phirimo, ndi kulipatula.

24 Ndipo Yehova anati kwa iye, Muka, tsika: nukwere iwe ndi Aroni pamodzi ndi iwe; koma ansembe ndi anthu asapyole kukwera kwa Yehova, angawapasule.

25 Pamenepo Mose anawatsikira anthu, nanena nao.