Eksodo 29 BL92

Mapatulidwe a ansembe

1 Ici ndico uwacitire kuwapatula, andicitire nchito ya nsembe: tenga ng'ombe yamphongo, ndi nkhosa ziwiri zamphongo zangwiro,

2 ndi mkate wopanda cotupitsa, ndi timitanda topanda cotupitsa tosanganiza ndi mafuta, ndi timitanda taphanthi topanda cotupitsa, todzoza ndi mafuta; utipange ndi ufa wosalala watirigu.

3 Ndipo uziike mu mtanga umodzi, ndi kubwera nazo mumtanga, pamodzi ndi ng'ombe yamphongo ndi nkhosa ziwiri zamphongo.

4 Ndipo ubwere nao Aroni ndi ana ace amuna ku khomo la cihema cokomanako indi kuwasambitsa m'madzi.

5 Pamenepo utenge zobvalazo ndi kubveka Aroni maraya am'kati, ndi mwinjiro wa efodi, ndi efodi, ndi capacifuwa, ndi kummangira m'cuuno ndi mpango wa efodi woluka mwanzeru;

6 ndipo uike nduwira pamutu pace, ndi kuika korona wopatulika panduwirapo.

7 Pamenepo utenge mafuta odzoza nao nuwatsanulire pamutu pace, ndi kumdzoza.

8 Ndipo ubwere nao ana ace amuna ndi kuwabveka maraya am'kati.

9 Uwamangirenso Aroni ndi ana ace amuna mipango m'cuuno mwao, nuwamangire akapa pamutu pao; ndipo akhale ansembe mwa lemba losatha; nudzaze dzanja la Aroni ndi dzanja la ana ace amuna,

10 Ndipo ubwere nayo ng'ombe yamphongo patsogolo pa cihema cokomanako; ndipo Aroni ndi ana ace amuna aike manja ao pamutu pa ng'ombe yamphongoyo.

11 Nuphe ng'ombe yamphongoyo pamaso pa Yehova, pa khomo la cihema cokomanako.

12 Pamenepo utapeko pa mwazi wa ng'ombe yamphongo, ndi kuupaka pa nyanga za guwa la nsembe ndi cala cako, nutsanulire mwazi wonse pa tsinde la guwa la nsembe.

13 Nutenge mafuta onse akukuta matumbo, ndi cokuta ca mphafa ndi imso ziwiri, ndi mafuta ali pa izo, ndi kuzitentha pa guwa la nsembe.

14 Koma nyama ya ng'ombeyo, ndi cikopa cace, ndi cipwidza cace, uzitentha izi ndi moto kunja kwa cigono; ndiyo nsembe yaucimo.

15 Utengenso nkhosa yamphongo imodziyo; ndi Aroni ndi ana ace amuna aike manja ao pamutu pa nkhosa yamphongoyo.

16 Nuiphe nkhosa yamphongoyo, ndi kutenga mwazi wace, ndi kuuwaza pa guwa la nsembe pozungulira.

17 Ndipo upadzule nkhosa yamphongo m'ziwalo zace, ndi kutsuka matumbo ace, ndi miyendo yace, ndi kuziika pa ziwalo zace, ndi pamutu pace.

18 Pamenepo upsereze, nkhosa yamphongo yonse pa guwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza ya Yehova, ya pfungo lokoma; ndiyo nsembe yamoto ya Yehova.

19 Ndipo utenge nkhosa yamphongo yinayo; ndi Aroni ndi ana ace amuna aike manja ao pamutu pa nkhosa yamphongoyo.

20 Pamenepo uiphe nkhosa yamphongoyo, nutapeko pa mwazi wace, ndi kuupaka pa ndewerere ya khutu lamanja la Aroni, ndi pa ndewerere ya khutu lamanja la ana ace amuna, ndi pa cala cacikulu ca dzanja lao lamanja, ndi pa cala cacikulu ca phazi lao lamanja, ndi kuuwaza mwaziwo pa guwa la nsembe posungulira,

21 Ndipo utapeko pamwazi uli pa guwa la nsembe, ndi pa mafuta akudzoza nao, ndi kuwaza pa Aroni, ndi pa zobvala zace, ndi pa ana ace amuna, ndi pa zobvala za ana ace amuna, pamodzi ndi iye; kuti akhale wopatulidwa, ndi zobvala zace zomwe, ndi ana ace amuna ndi zobvala zao zomwe pamodzi ndi iye.

22 Utengenso mafuta a nkhosa yamphongoyo, ndi me ira, ndi mafuta akukuta mat umbo, ndi cokuta ca mphafa, ndi imso ziwiri, ndi mafuta ali pamenepo, ndi mwendo wam'mwamba wa ku dzanja lamanja; pakuti ndiyo nkhosa yamphongo ya kudzaza manja;

23 ndi mkate wamphumphu umodzi, ndi kamtanda ka mkate wosanganiza ndi mafuta, ndi kamtanda kamodzi kaphanthi, ziri mu mtanga wa mkate wopanda cotupitsa wokhala pamaso pa Yehova;

24 ndipo uike zonsezo m'manja a Aroni, ndi m'manja a ana ace amuna; nuziweyule nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.

25 Pamenepo uzilandire m'manja mwao, ndi kuzipsereza pa guwa la nsembe, pa nsembe yopsereza, zicite pfungo lokoma pamaso pa Yehova; ndiyo nsembe yamoto ya Yehova.

26 Ndipo utenge nganga ya nkhosa yamphongo yodzaza manja ya Aroni, ndi kuiweyula ikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndipo ikhale gawo lako.

27 Ndipo upatule nganga va nsembe yoweyula, ndi mwendo wam'mwamba wa nsembe yokweza, imene anaiweyula, ndi imene anaikweza, za nkhosa yamphongo yakudzaza manja; ziri za Aroni, ndi za ana ace amuna;

28 ndipo zikhale za Aroni ndi za ana ace amuna, mwa lemba losatha, ziwadzere kwa ana a Israyeli; popeza ndiyo nsembe yokweza; ndipo ikhale nsembe yokweza yodzera kwa ana a Israyeli, ya kwa nsembe zamtendere zao, ndiyo nsembe yao yokweza ya Yehova.

29 Ndipo zobvala zopatulika za Aroni zikhale za ana ace amuna pambuyo pace, kuti awadzoze atazibvala, nadzaze manja ao atazibvala;

30 mwana wace wamwamuna amene adzakhala wansembe m'malo mwace azibvala masiku asanu ndi awiri, pakulowa iye m'cihema cokomanako kutumikira m'malo opatulika.

31 Ndipo utenge nkhosa yamphongo yodzaza manja, nuphike nayama yace m'malo opatulika.

32 Ndipo Aroni ndi ana ace amuna adye nyama ya nkhosa yamphongoyo, ndi mkate uli mumtanga, pa khomo la cihema cokomanako.

33 Ndipo adye zimene anacita nazo coteteza, kuti awadzaze manja ndi kuwapatulitsa; koma mlendo asadyeko, pakuti nzopatulika izi.

34 Ndipo ikatsalako nyama yodzaza manja, kapena mkate kufikira m'mawa, pamenepo utenthe zotsalazo ndi moto; asazidye popeza ncopatulika ici.

35 Ndipo utero nao Aroni, ndi ana ace amuna, monga mwa zonse ndakuuza; udzaze manja ao masiku asanu ndi awiri.

36 Nukonze ng'ombe yamphongo, ndiyo nsembe yaucimo yakuteteza nayo, tsiku ndi tsiku; ndipo uyeretsa guwa la nsembe, pakucita coteteza pamenepo; ndipo ulidzoze kulipatula.

37 Ucitire guwa la nsembe coteteza masiku asanu ndi awiri ndi kulipatula; ndipo a guwa la nsembelo likhale lopatulikitsa; ciri conse cikhudza guwa la nsembelo cikhale copatulika.

Nsembe ya masiku onse

38 Koma izi ndizo uzikonza pa guwa la nsembelo; ana a nkhosa awiri a caka cimodzi, tsiku ndi tsiku kosalekeza.

39 Mwana wa nkhosa wina ukonze m'mawa; ndi mwana wa nkhosa wina ukonze madzulo;

40 ndi pa mwana wa nkhosa mmodziyo pakhale limodzi la magawo khumi la ufa wosalala, wosanganiza ndi limodzi la magawo anai la hini wa mafuta opera; ndi limodzi la magawo anai la hini wa vinyo, likhale nsembe yothira.

41 Ndi mwana wa nkhosa wina ukonze madzulo; umkonze umo unacitira copereka ca m'mawa ndi nsembe yace yothira, akhale pfungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova.

42 Ikhale nsembe yopsereza yosalekeza ya mwa mibadwo yanu, pa khomo la cihema cokomanako, pamaso pa Yehova, kumene ndidzakomana nanu, kulankhula nawe komweko.

43 Ndipo pamenepo ndidzakomana ndi ana a Israyeli; ndipo cihema cidzapatulidwa ndi ulemerero wanga.

44 Ndipo ndidzapatula cihema cokomanako, ndi guwa la nsembe; ndidzapatulanso Aroni ndi ana ace amuna omwe, andicitire nchito ya nsembe.

45 Ndipo ndidzakhala pakati pa ana a Israyeli, ndi kukhala Mulungu wao.

46 Ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, amene ndinawaturutsa m'dziko la Aigupto, kuti ndikhale pakati pao. Ine ndine Yehova Mulungu wao.