Eksodo 14 BL92

Farao alondola Aisrayeli

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

2 Lankhula ndi anthu a Israyeli kuti abwerere m'mbuyo nagone patsogolo pa Pihahiroti, pakati pa Migidoli ndi nyanja yamcere, patsogolo pa Baala-Zefoni; pandunji pace mugone panyanja.

3 Ndipo Farao adzanena za ana a Israyeli, Azimidwa dziko, cipululu cawatsekera.

4 Ndipo ndidzalimbitsa mtima wace wa Farao kuti awalondole; ndipo ndidzalemekezedwa pa Farao ndi pa nkhondo yace yonse; pamenepo Aaigupto adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, Ndipo anacita comweco.

5 Ndipo anauza mfumu ya Aigupto kuti anthu adathawa; ndi mtima wa Farao ndi wa anyamata ace inasandulikira anthuwo, ndipo anati, Ici nciani tacita, kuti talola Israyeli amuke osatigwiriranso nchito?

6 Ndipo anamanga gareta lace, napita nao anthu ace;

7 napita nao magareta osankhika mazana asanu ndi limodzi, ndi magareta onse a m'Aigupto, ndi akapitao ao onse.

8 Ndipo Yehova analimbitsa mtima wa Farao, mfumu ya Aigupto, ndipo iye analondola ana a Israyeli; koma ana a Israyeli adaturuka ndi dzanja lokwezeka.

9 Ndipo Aaigupto anawalondola, ndiwo akavalo ndi magareta onse a Farao, ndi apakavalo ace, ndi nkhondo yace, nawapeza ali kucigono kunyanja, pa Pihahiroti, patsogolo pa Baala-Zefoni.

10 Ndipo pamene Farao anayandikira ana a Israyeli anatukula maso ao, taonani, Aaigupto alinkutsata pambuyo pao; ndipo anaopa kwambiri; ndi ana a Israyeli anapfuulira kwa Yehova.

11 Ndipo anati kwa Mose, Kodi mwaticotsera kuti tikafe m'cipululu cifukwa panahbe manda m'Aigupto? Nciani ici mwaticitira kuti mwatiturutsa m'Aigupto?

12 Si awa maowo tinalankhula nanu m'Aigupto ndi kuti, Tliekeni, kuti tigwirire nchito Aaigupto? pakuti kutumikira Aaigupto kutikomera si kufa m'cipululu ai.

13 Ndipo Mose ananena ndi anthu, Musaope, cirimikani, ndipo penyani cipulumutso ca Yehova, cimene adzakucitirani lero; pakuti Aaigupto mwawaona lerowa simudzawaonansokonse.

14 Yehova adzakugwirirani nkhondo, ndipo inu mudzakhala cere.

Aisrayeli aoloka pouma

15 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Upfuuliranji kwa Ine? lankhula ndi ana a Israyeli kuti aziyenda.

16 Ndipo iwe nyamula ndodo yako, nutambasulire dzanja lako kunyanja, nuigawe, kuti ana a Israyeli alowe pakati pa nyanja pouma.

17 Ndipo Ine, taonani, ndilimbitsa mitima ya Aaigupto, kuti alowemo powatsata; ndipo ndidzalemekezedwa pa Farao, ndi pa nkhondo yace yonse, pa magareta ace, ndi pa okwera pa akavalo ace.

18 Ndipo Aaigupto adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, polemekezedwa Ine pa Farao, pa magareta ace, ndi pa okwera pa akavalo ace.

19 Ndipo mthenga wa Mulungu, wakutsogolera ulendo wa Israyeli, unacokako, nutsata pambuyo pao; ndipo mtambo njo uja unacoka patsogolo pao, nuima pambuyo pao;

20 nulowa pakati pa ulendo wa Aaigupto ndi ulendo wa Aisrayeli ndipo mtambo unacita mdima, komanso unaunikira usiku; ndipo ulendo wina sunayandikizana ndi unzace usiku wonse.

21 Ndipo Mose anatambasulira dzanja lace kunyanja; ndipo Yehova anabweza nyanja ndi mphepo yolimba ya kum'mawa usiku wonse, naumitsa nyanja; ndipo madziwo anagawikana.

22 Ndipo ana a Israyeli analowa pakati pa nyanja pouma; ndi madziwo anakhala kwa iwo ngati khoma palamanja, ndi palamanzere.

23 Ndipo Aaigupto anawalondola, nalowa pakati pa nyanja powatsata, ndiwo akavalo onse a Farao, magareta ace, ndi apakavalo ace.

24 Ndipo kunali, ulonda wa mamawa, Yehova ali m'moto ndi m'mtambo njo anapenyera pa ulendo wa Aaigupto, Baubvuta ulendo wa Aaigupto.

25 Ndipo anagurula njinga za magareta ao, nawayendetsa molemetsa; pamenepo Aaigupto anati, Tithawe pamaso pa Israyeli; pakuti Yehova alikuwagwirira nkhondo pa Aaigupto.

Aaigupto amizidwa m'nyanja

26 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tambasulira dzanja lako kunyanja, kuti madziwo abwerere kudzamiza Aaigupto, magareta ao, ndi apakavalo ao.

27 Ndipo Mose anatambasulira dzanja lace kunyanja, ndi nyanja inabwerera m'mayendedwe ace mbanda kuca; ndipo Aaigupto pothawa anakomana nayo; ndipo Yehova anakutumula Aaigupto m'kati mwa nyanja.

28 Popeza madziwo anabwerera, namiza magareta ndi apakavalo, ndiwo nkhondo yonse ya Farao imene idalowa pambuyo pao m'nyanja; sanatsala wa iwowa ndi mmodzi yense.

29 Koma ana a Israyeli anayenda pouma pakati pa nyanja; ndi madziwo anakhala ngati khoma kwa iwo, palamanja ndi palamanzere.

30 Comweco Yehova anapulumutsa Israyeli tsiku lomwelo m'manja a Aaigupto; ndipo Israyeli anaona Aaigupto akufa m'mphepete mwa nyanja.

31 Ndipo Israyeli anaiona nchito yaikuru imene Yehova anacitira Aaigupto, ndipo anthuwo anaopa Yehova; nakhulupirira Yehova ndi mtumiki wace Mose.