Eksodo 38 BL92

Mapangidwe a guwa la nsembe yopsereza

1 Ndipo anapanga guwa la nsembe yopsereza la mtengo wasitimu; utali wace mikono isanu, ndi kupingasa kwace mikono isanu, lampwamphwa; ndi msinkhu wace mikono itaru.

2 Ndipo anapanga nyanga zace pa ngondya zace zinai; nyanga zace zinakhala zoturuka m'mwemo; ndipo analikuta ndi mkuwa.

3 Anapanganso zipangizo zonse za guwalo, zotayira, ndi zoolera, ndi mbale zowazira, ndi mitungo, ndi zoparira moto; zipangizo zace zonse anazipanga zamkuwa.

4 Ndipo anapangira guwa La nsembelo made, malukidwe ace nja mkuwa, pansi pa matso ace wakulekeza pakati pace.

5 Ndipo anayengera mathungo anai a made amkuwawo mphete zinai, zikhale zopisamo mphiko.

6 Napanga mphiko za mtengo wasitimu, nazikuta ndi mkuwa.

7 Ndipo anapisa mphikozo m'zimphetemo pa mbali za guwa la nsembe, kulinyamulira nazo; analipanga ndi matabwa, lagweregwere.

8 Ndipo anapanga mkhate wamkuwa, ndi tsinde lace lamkuwa, wa akalirole a akazi otumikira, akutumikira pa khomo la cihema cokomanako.

Bwalo La cihema

9 Ndipo anapanga bwalo; pa mbali ya kumwela, kumwela, nsaru zocingira za pabwalo zinali za bafuta wa thonje losansitsa, mikono zana limodzi;

10 nsici zace makumi awiri, ndi makamwa ao makumi awiri, amkuwa; zokowera za nsici ndi mitanda yace zasiliva.

11 Ndi pa mbali ya kumpoto mikono zana limodzi, nsici zace makumi awiri, nw makamwa ace makumi awiri, amkuwa; zokowera za nsici ndi mitanda yace yasiliva.

12 Ndi pa mbali ya kumadzulo panali nsaru zocingira za mikono makumi asanu, nsid zace khumi, ndi makamwa ace khumi; zokowera za nsici ndi mitanda yace yasiliva.

13 Ndi pa mbali ya kum'mawa, kum'mawa, mikono makumi asanu.

14 Nsaru zocingira za pa mbali imodzi ya cipata nza mikono khumi ndi isanu; nsici zace zitatu, ndi makamwa ace atatu;

15 momwemonso pa mbali yina: pa mbali yino ndi pa mbali yina ya cipata ca pabwalo panali nsaru zocingira za mikono khumi ndi isanu; nsici zace zitatu, ndi makamwa ace atatu.

16 Nsaru zocingira zonse za pabwalo pozungulira zinali za bafuta wa thonje losansitsa.

17 Ndipo makamwa a nsici anali amkuwa; zokowera za nsici ndi mitanda Iyace zasiliva; ndi zokutira mitu yace zasiliva; ndi nsici zonse za pabwalo zinagwirana pamodzi ndi siliva.

18 Ndi nsaru yotsekera pa cipata ca pabwalo ndiyo nchito ya wopikula, ya lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa; utali wace mikono makumi awiri, ndi msinkhu wace mu kupingasa kwace mikono isanu, yolingana ndi nsaru zocingira za pabwalo.

19 Ndi nsici zace zinali zinai, ndi makamwa ace anai, amkuwa; zokowera zace zasiliva, ndi zokutira mitu yace ndi mitanda yace zasiliva.

20 Ndi ziciri zonse za cihema, ndi za bwalo lace pozungulira, nza mkuwa.

Mawerengo a zopereka za pa cihemao

21 Ici ndi ciwerengo ca zinthu za cihema, cihema ca mboni, monga anaziwerenga, monga mwa mau a Mose, acite nazo Alevi; anaziwerenga Itamara, mwana wa Aroni wansembe.

22 Ndipo Bezaleli mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa pfuko la Yuda, anapanga zonse zimene Mulungu adauza Mose.

23 Ndi pamodzi naye Aholiabu, mwana wa Ahisama, wa pfuko la Dani, ndiye wozokota miyala, ndi mmisiri waluso, ndiponso wopikula ndi lamadzi ndi lofiira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.

24 Golidi yense anacita naye mu nchito yonse ya malo opatulika, golidi wa coperekaco, ndico matalente makumi awiri kudza asanu ndi anai, ndi masekeli mazana asanu ndi awiri, kudza makumi atatu, monga mwa sekeli wa malo opatulika.

25 Ndipo siliva wa iwo owerengedwa a khamulo ndiwo matalente zana limodzi, ndi masekeli cikwi cimodzi, kudza mazana asanu ndi awiri, mphambu makumi asanu ndi awiri kudza asanu, kuyesa sekeli wa malo opatulika;

26 munthu mmodzi anapereka beka, ndiwo limodzi la magawo awiri la sekeli, kuyesa sekeli wa malo opatulika, anatero onse akupita kumka kwa owerengedwawo, kuyambira munthu wa zaka makumi awiri ndi oposa, ndiwo anthu zikwi mazana asanu ndi limodzi kudza zitatu, ndi mazana asanu mphambu makumi asanu.

27 Ndipo matalente zana limodzi a siliva ndiwo a kuyengera makamwa a malo opatulika, ndi makamwa a nsaru yocinga; makamwa zana limodzi matalente zana limodzi, talente limodzi kamwa limodzi.

28 Ndipo anapanga zokowera za mizati nsanamira ndi nsici ndi masekeli aja cikwi cimodzi kudza mazana asanu ndi awiri mphambu asanu, nakuta mitu yace, nazigwirizitsana pamodzi.

29 Ndi mkuwa wa coperekaco ndiwo matalente makumi asanu ndi awiri, ndi masekeli zikwi ziwiri kudza mazana anai.

30 Ndipo anapanga nao makamwa a pa khomo la cihema cokomanako, ndi guwa la nsembe lamkuwa, ndi made ace amkuwa, ndi zipangizo zonse za guwa la nsembe,

31 ndi makamwa a pabwalo pozungulira, ndi makamwa a ku cipata ca pabwalo, ndi ziciri zonse za cihema, ndi ziciri zonse za pabwalo pozungulira.