Eksodo 12 BL92

Kuikidwa kwa Paskha

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni m'dziko la Aigupto, ndi kuti,

2 Mwezi uno uzikhala kwa inu woyamba wa miyezi; muziuyesa mwezi woyamba wa caka.

3 Mulankhule ndi msonkhano wonse wa Israyeli ndi kuti, Tsiku lakhumi la mwezi uno adzitengere munthu yense mwana wa nkhosa, monga mwa mabanja a atate ao, mwana wa nkhosa pabanja.

4 Banja likaperewera mwana wa nkhosa, munthu ndi mnzace ali pafupi pa nyumba yace atenge monga mwa kufikira kwa anthu ao; muziwerengera mwana wa nkhosa monga mwa kudya kwao.

5 Mwana wa nkhosa wanu azikhala wangwiro, wamwamuna, wa caka cimodzi; muzimtenga ku nkhosa kapena ku mbuzi.

6 Ndipo mukhale naye cisungire kufikira tsiku lakhumi ndi cinai la mwezi womwe; ndipo bungwe lonse la anthu a Israyeli lizimupha madzulo.

7 Ndipo azitengako mwazi, naupake pa mphuthu za mbali ndi ya pamwamba m'nyumba zimene adyeramo.

8 Ndipo azidya nyamayo usiku womwewo, yooca pamoto, ndi mkate wopanda cotupitsa; aidye ndi ndiwo zowawa,

9 Musaidya yaiwisi, kapena yophika ndi madzi konse ai, koma yooca pamoto; muti wace ndi miyendo yace ndi matumbo ace.

10 Ndipo musasiyako kufikira m'mawa; koma yotsalira kufikira m'mawayo muipsereze ndi moto:

11 Ndipo muziidya cotero: okwinda m'cuuno, nsapato zanu pa mapazi anu ndodo yanu m'dzanja lanu, ndipo muziidya msanga; ndiye Paskha wa Yehova.

12 Pakuti ndidzapita pakati pa dziko la Aigupto usiku womwewo, ndi kukantha ana oyamba onse m'dziko la Aigupto, anthu ndi zoweta; ndipo ndidzacita maweruzo pa milungu yonse ya Aigupto; Ine ndine Yehova.

13 Ndipo mwaziwo udzakhala cizindikilo kwa inu pa nyumba zimene mukhalamo; pamene ndiona mwaziwo ndidzapitirira inu, ndipo sipadzakhala mliri wakukuonongani, pakukantha Ine dziko la Aigupto,

14 Ndipo tsiku lino lidzakhala kwa inu cikumbutso, muzilisunga la madyerero a Yehova; ku mibadwo yanu muzilisunga la madyerero, likhale lemba losatha.

15 Masiku asanu ndi awiri muzidya mkate wopanda cotupitsa; lingakhale tsiku loyamba muzicotsa cotupitsa m'nyumba zanu; pakuti ali yense wakudya mkate wa cotupitsa kuyambira tsiku loyamba kufikira tsiku lacisanu ndi ciwiri, munthu amene adzasadzidwa kwa Israyeli.

16 Ndipo tsiku loyamba kukhale kusonkhana kopatulika, ndi tsiku lacisanu ndi ciwiri kukhalenso kusonkhana kopatulika; pasacitike nchito masikuwo, zokhazi zakudya anthu onse ndizo muzicita.

17 Ndipo muzisunga madyerero a mkate wopanda cotupitsa; pakuti tsiku lomwe lino ndinaturutsa makamu anu m'dziko la Aigupto; cifukwa cace muzisunga tsiku lino m'mibadwo yanu, lemba losatha.

18 Mwezi woyamba, tsiku lace lakhumi ndi cinai madzulo ace, muzidya mkate wopanda cotupitsa, kufikira tsiku la makumi awiri mphambu limodzi la mwezi, madzulo ace.

19 Cisapezeke cotupitsa m'nyumba zanu masiku asanu ndi awiri; pakuti ali yense wakudya kanthu ka cotupitsa, munthuyo adzasadzidwa ku msonkhano wa Israyeli, angakhale ndiye mlendo kapena wobadwa m'dziko.

20 Musadye kanthu ka cotupitsa; mokhala inu monse muzidya mkate wopandacotupitsa.

21 Pamenepo Mose anaitana akuru onse a Israyeli, nanena nao, Pitani, dzitengereni ana a nkhosa monga mwa mabanja anu, nimuphere Paskha.

22 Ndipo muzitenga mpukutu wa hisope, ndi kuubviika m'mwazi uli m'mbale, ndi kupaka mwazi uli m'mbalemo pa mphuthu ya pamwamba ndi pambali; koma inu, asaturuke munthu pakhomo pa nyumba yace kufikira m'mawa.

23 Pakuti Yehova adzapita pakatipo kukantha Aaigupto; koma pamene adzaona mwaziwo pa mphuthu pamwamba ndi za pambali, Yehova adzapitirira pakhomopo, osalola woonongaalowe m'nyumba zanu kukukanthani.

24 Ndipo muzisunga cinthu ici cikhale lemba la kwa inu, ndi kwa ana anu ku nthawi zonse.

25 Ndipo kudzakhala, pamene mulowa m'dziko limene Yehova adzakupatsani, mensa analankhula, muzisunga kutumikira kumeneku.

26 Ndipo kudzakhala, pamene ana anu adzanena ndi inu, Kutumikiraku muli nako nkutani?

27 mudzati, Ndiko nsembe ya Paskha wa Yehova, amene anapitirira nyumba za ana a Israyeli m'Aigupto, pamene anakantha Aaigupto, napulumutsa nyumba zathu.

28 Ndipo anthu anawerama, nalambira. Ndipo ana a Israyeli anamuka nacita monga Yehova adalamulira Mose ndi Aroni; anacita momwemo.

Ana oyamba kubadwa aphedwa

29 Ndipo panakhala pakati pa usiku, Yehova anakantha ana oyamba onse a m'dziko la Aigupto, kuyambira mwana woyamba wa Earao wakukhala pa mpando wacifumu wace kufikira mwana woyamba wa wam'nsinga ali m'kaidi; adi ana oyamba onse a zoweta.

30 Ndipo Farao anauka usiku, iyendi anyamata ace onse, ndi Aaigupto onse; ndipo kunali kulira kwakukulu m'Aigupto; pakuti panalibe nyumba yopanda wakufa m'mwemo.

31 Ndipo anaitana Mose ndi Aroni usiku, nati, Ukani, turukani pakati pa anthu anga, inu ndi ana a Israyeli; ndipo mukani katumikireni Yehova, monga mwanena.

32 Muka nazoni zoweta zanu zazing'ono ndi zazikuru, monga mwanena; cokani, ndi kundidalitsa Inenso.

33 Ndipo Aaigupto anaumiriza anthuwo, nafulumira kuwaturutsa m'dziko; pakuti anati, Tiri akufa tonse.

34 Ndipo anthu anatenga mtanda wao usanatupe, ndi zoumbiramo zao zomangidwa m'zobvala zao pa mapewa ao.

35 Ndipo ana a Israyeli anacita monga mwa mau a Mose; napempha Aaigupto zokometsera zasiliva, ndi zagolidi, ndi zobvala.

36 Ndipo Yehova anapatsa anthu cisomo pamaso pa Aaigupto, ndipo sanawakaniza. Ndipo anawafunkhira Aaigupto.

Ana a Israyeli aturuka m'Aigupto

37 Ndipo ana a Israyeli anayenda ulendo wakucokera ku Ramese kufikira ku Sukoti, zikwi mazana asanu ndi limodzi oyenda okha, ndiwo amuna, osawerenga ana.

38 Ndipo anthu ambiri osokonezeka anakwera nao; ndi nkhosa ndi ng'ombe, zoweta zambirimbiri.

39 Ndipo anaoca timitanda topanda cotupitsa ta mtanda umene anabwera nao ku Aigupto, popeza sadaikamo cotupitsa; pakuti adawapitikitsa ku Aigupto, ndipo sanathe kucedwa, kapena kudzikonzeratu kamba.

40 Ndipo kukhala kwa ana a Israyeli anakhala m'Aigupto ndiko zaka mazana anai kudza makumi atatu.

41 Ndipo kunakhala pakutha zaka mazana anai kudza makumi atatu, inde panakhala tsiku lomwelo, makamu onse a Yehova anaturuka m'dziko la Aigupto.

42 Ndiwo usiku wosungira Yehova ndithu, cifukwa ca kuwaturutsa m'dziko la Aigupto; usiku womwe uno ukhale wosungira Yehova ana onse a Israyeli ku mibadwo yao.

Lamulo la Paskha

43 Ndipo Yehova anati kwa Mose ndi Aroni, Lemba la Paskha ndi ili: mwana wa mlendo ali yense asadyeko;

44 koma kapolo wa mwini ali yense, wogula ndi ndarama, utamdula, ndipo adyeko.

45 Mlendo kapena wolembedwa nchito asadyeko.

46 Audye m'nyumba imodzi; usaturukira nayo kubwalo nyama yina; ndipo musathyole pfupa lace.

47 Msonkhano wonse wa Israyeli uzicita ici.

48 Koma akakhala nanu mlendo, nakonzera Yehova Paskha, adulidwe amuna ace onse, ndipo pamenepo asendere kuucita; nakhale ngati wobadwa m'dziko; koma wosadulidwa ali yense asadyeko.

49 Pakhale lamulo lomweli pa wobadwa m'dziko, ndi pa mlendo wakukhala pakati pa inu.

50 Ndipo ana onse a Israyeli anacita monga Yehova adawalamulira Mose ndi Aroni, momwemo anacita.

51 Ndipo kunakhala tsiku lomwelo, kuti Yehova anaturutsa ana a Israyeli m'dziko la Aigupto, monga mwa makamu ao.