Eksodo 2 BL92

Kubadwa kwa Mose

1 Ndipo anamuka munthu wa banja la Levi, natenga mwana wamkazi wa Levi.

2 Ndipo anaima mkaziyo, naonamwanawamwamuna; m'mene anamuona kuti ali wokoma, anambisa miyezi itatu.

3 Koma pamene sanathe kumbisanso, anamtengera kabokosi kagumbwa, napakapo nkhunga ndi phula; naikamo mwanayo, nakaika pakati pa mabango m'mbali mwa nyanja.

4 Ndipo mlongo wace anaima patali, adziwe comwe adzamcitira.

5 Ndipo mwana wamkazi wa Farao anatsikira kukasamba m'nyanja; ndipo atsikana ace anayendayenda m'mbali mwa nyanja; ndipo iye anaona kabokosi pakati pa mabango, natuma mdzakazi wace akatenge.

6 Pamene anakabvundukula, anapenya mwanayo; ndipo, taonani, khandalo lirikulira. Ndipo anamva naye cifundo, nati, Uyu ndiye wa ana a Ahebri.

7 Pamenepo mlongo wace ananena ndi mwana wamkazi wa Farao, Ndipite ine kodi kukuitanirani woyamwitsa wa Ahebri, akuyamwitsireni mwanayo?

8 Ndipo mwana wamkazi wa Farao ananena naye, Pita. Napita namwaliyo, nakaitana amace wa mwanayo.

9 Ndipo mwana wamkazi wa Farao ananena naye, Pita naye mwana uyu, ndi kundiyamwitsira iye, ndidzakupatsa mphotho yako. Ndipo mkaziyo anatenga mwanayo, namyamwitsa,

10 Ndipo atakula mwanayo, anapita naye kwa mwana wamkazi wa Farao, ndipo iye anakhala mwana wace. Ndipo anamucha dzina lace Mose, nati, Cifukwa ndinambvuula m'madzi.

11 Ndipo kunali masiku amenewo, atakula Mose, kuti anaturukira kukazonda abale ace, napenya akatundu ao; ndipo anaona munthu M-aigupto ali kukantha Mhebri, wa abale ace.

12 Ndipo anaunguza kwina ndi kwina, ndipo pamene anaona kuti palibe munthu, anakantha M-aigupto, namfotsera mumcenga.

13 M'mawa mwace anaturukanso, ndipo, taonani, anthu awiri Ahebri alikugwirana; ndipo ananena ndi wocimwayo, kuti, Umpandiranji mnzako?

14 Koma anati, Wakuika iwe ndani ukhale mkuru ndi woweruza wathu? kuteroku ukuti undiphe, monga unamupha M-aigupto? Ndipo Mose anacita mantha, nanena, Ndithu cinthuci cadziwika.

15 Pamene Farao anacimva ici, anafuna kupha Mose. Koma Mose anathawa pankhope pa Farao, nakhala m'dziko la Midyani; nakhala pansi pacitsime.

16 Ndipo wansembe wa Midyani anali nao ana akazi asanu ndi awiri, amene anadza kudzatunga madzi; ndipo anadzaza mimweco kuti amwetse gulu la atate wao.

17 Pamenepo anadza abusa nawapitikitsa; koma Mose anauka nawathandiza, namwetsa gulu lao.

18 M'mene anafika kwa Rehueli atate wao, iye anati, Mwabwera msanga bwanji lero?

19 Ndipo anati two, Munthu M-aigupto anatilanditsa m'manja a abusa, natitungiranso madzi okwanira, namwetsa gululi.

20 Ndipo anati kwa ana ace akazi, Ali kuti iye? Mwamsiyiranji munthuyo? Kamuitaneni, adzadye cakudya.

21 Ndipo Mose anabvomera kukhala naye munthuyo; ndipo anampatsa Mose mwana wace wamkazi Zipora.

22 Ndipo anaona mwana, ndi Mose anamucha dzina lace Gerisomu; pakuti anati, Ndakhala mlendo m'dziko la eni.

23 Ndipo kunali pakupita masiku ambiri aja, idafa mfumu ya Aigupto; ndi ana a Israyeli anatsitsa moyo cifukwa ca ukapolo wao, nalira, ndi kulira kwao kunakwera kwa Mulungucifukwa ca ukapolowo.

24 Ndipo Molungu anamva kubuula kwao, ndi Mulungu anakumbukila cipangano cace ndi Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo.

25 Ndipo Molungu anapenya Aisrayeli, ndi Mulungu anadziwa.