1 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Lowa kwa Farao; pakuti ndaumitsa mtima wace, ndi mtima wa anyamata ace, kuti ndiike zizindikilo zanga izi pakati pao;
2 ndi kuti ufotokozere, m'makutu a ana ako, ndi a zidzukulu zako, comwe ndidzacita m'Aigupto, ndi zizindikilo zanga zimene ndinaziika pakati pao; kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova.
3 Ndipo Mose ndi Aroni analowa kwa Farao nanena naye, Atero Yehova, Mulungu wa Ahebri, Ukana kudzicepetsa pamaso panga kufikira liti? Lola anthu anga amuke, akanditumikire;
4 pakuti ukakana kulola anthu anga amuke, taona, mawa ndidzafikitsa dzombe m'dziko lako;
5 ndipo lidzakuta nkhope ya dziko, kotero, kuti palibe munthu adzakhoza kuona dziko; ndipo lidzadya zotsalira zidapulumuka, zidatsalira inu pamatalala, ndipo lidzadya mtengo uti wonse wokuphukirani kuthengo;
6 ndipo lidzadzaza m'nyumba zako, ndi m'nyumba za anyamata ako onse, ndi m'nyumba za Aaigupto onse; sanaciona cotere atate ako kapena makolo ako, kuyambira tsiku lija lakukhala iwo pa dziko lapansi kufikira lero lino. Ndipo anatembenuka, naturuka kwa Farao.
7 Ndipo anyamata ace a Farao ananena naye, Ameneyo amaticitira msampha kufikira liti? Lolani anthuwo amuke, akatumikire Yehova Mulungu wao. Kodi simunayambe kudziwa kuti Aigupto laonongeka?
8 Ndipo anawabwereretsa Mose ndi Aroni kwa Farao, nanena nao, Mukani, katumikireni Yehova Mulungu wanu. Koma amene adzapitawo ndiwo ani?
9 Ndipo Mose anati, Tidzamuka ndi ana athu ndi akuru athu, ndi ana athu amuna ndi akazi; tidzamuka nazo nkhosa zathu ndi ng'ombe zathu; pakuti tiri nao madyerero a Yehova.
10 Ndipo ananena nao, Momwemo, Yehova akhale nanu ngati ndilola inu ndi ana ang'ono anu mumuke; cenjerani, pakuti pali coipa pamaso panu,
11 Cotero ai, mukani tsopano, inu amuna akuru, tumikirani Yehova pakuti ici mucifuna. Ndipo anawapitikitsa pamaso pa Farao.
12 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tambasulira dzanja lako pa dziko la Aigupto, lidze dzombe, kuti likwere pa dziko la Aigupto, lidye zitsamba zonse za m'dziko, ndizo zonse adazisiya matalala.
13 Pamenepo Mose analoza ndodo yace pa dziko la Aigupto; ndipo Yehova anaombetsa padziko mphepo ya kum'mawa usana wonse, ndi usiku womwe; ndipo kutaca mphepo ya kum'mawa inadza nalo dzombe.
14 Ndipo dzombe linakwera pa dziko lonse la Aigupto, ndipo linatera pakati pa malire onse a Aigupto, lambirimbiri; lisanafike ili panalibe dzombe lotere longa ili, ndipo litapita ili sipadzakhalanso lotere.
15 Pakuti linakuta nkhope ya dziko lonse kuti dziko linada; ndipo linadya zitsamba zonse za m'dziko, ndi zipatso zonse za mitengo zimene matalala adazisiya; ndipo sipanatsala cabiriwiri ciri conse, pamitengo kapena pa zitsamba za kuthengo, m'dziko lonse la Aigupto.
16 Pamenepo Farao anafulumira kuitana Mose ndi Aroni; nati, Ndalakwira Yehova Mulungu wanu, ndi inu.
17 Ndipo tsopano, ndikhululukirenitu kulakwa kwanga nthawi yino yokha, nimundipembere kwa Yehova Mulungu wanu, kuti andicotsere imfa yino yokha.
18 Ndipo anaturuka kwa Farao, napemba Yehova.
19 Ndipo Yehova anabweza mphepo yolimbatu ya kumadzulo, imene inapita nalo dzombe niliponya m'Nyanja Yofiira: silinatsala dzombe limodzi pakati pa malire onse a Aigupto.
20 Koma Yehova analimbitsa mtima wa Farao, ndipo sanalola ana a Israyeli amuke.
21 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tambasulira dzanja lako kuthambo, ndipo padzakhala mdima pa dziko la Aigupto, ndiwo mdima wokhudzika.
22 Ndipo Mose anatambasulira dzanja lace kuthambo; ndipo munali mdima bii m'dziko lonse la Aigupto masiku atatu;
23 sanaonana, sanaukanso munthu pamalo pace, masiku atatu; koma kwa ana onse a Israyeli kudayera m'nyumba zao.
24 Ndipo Farao anaitana Mose, nati, Mukani, tumikirani Yehova; nkhosa zanu ndi ng'ombe zanu zokha zitsale; mumuke nao ana anu ang'ononso.
25 Koma Mose anati, Mutipatsenso m'dzanja mwathu nsembe zophera ndi nsembe zopsereza, kuti timkonzere Yehova Mulungu wathu.
26 Zoweta zathu zomwe tidzapita nazo; cosatsala ciboda cimodzi; pakuti mwa izo tiyenera kutenga zakutumikira nazo Yehova Mulungu wathu; ndipo tisanafikeko, sitidziwa umo tidzamtumikira Yehova.
27 Koma Yehova analimbitsa mtima wace wa Farao, ndipo anakana kuwaleka amuke.
28 Ndipo Farao ananena naye, Coka pano, uzicenjera usaonenso nkhope yanga; pakuti tsiku limene uonanso nkhope yanga udzafa.
29 Ndipo Mose anati, Mwanena bwino; sindidzaonanso nkhope yanu.