Eksodo 27 BL92

Za guwa la nsembe

1 Ndipo upange guwa la nsembe la mtengo wasitimu, utali wace mikono isanu, ndi kupingasa kwace mikono isanu, guwa la nsembelo likhale lampwamphwa, ndi msinkhu wace mikono itatu.

2 Ndipo uzipanga nyanga zace pa ngondya zace zinai; nyanga zace zikhale zoturuka m'mwemo: nulikute ndi mkuwa:

3 Ndipo uzipanga zotayira zace zakulandira mapulusa ace, ndi zoolera zace, ndi mbale zowazira zace, ndi mitungo yace, ndi zoparira moto zace; zipangizo zace zonse uzipanga zamkuwa.

4 Ndipo ulipangire made, malukidwe ace ndi amkuwa; nupange pa malukidwewo ngondya zace zinai mphete zinai zamkuwa.

5 Nuwaike pansi pa matso a guwa la nsembelo posungulira, kuti malukidwe alekeze pakati pa guwa la nsembelo.

6 Ndipo upangire guwa la nsembe mphiko, mphiko za mtengo wasitimu, ndi kuzikuta ndi mkuwa.

7 Ndipo apise mphiko m'mphetezo kuti mphikozo zikhale pa mbali ziwiri za guwa la nsembe polinyamula.

8 Ulipange lagweregwere ndi matabwa; monga anakuonetsa m'phirimo; alipange momwemo.

Za bwalo la cihema

9 Upangenso bwalo la cihema; pa mbali yace ya kumwela, kumwela, pakhale nsaru zocingira zakubwaloza nsaru ya bafuta wa thonje losansitsa, utali wace wa pa mbali imodzi mikono zana;

10 ndi nsici zace makumi awiri, ndi makamwa ao makumi awiri akhale amkuwa; zokowera za nsici ndi mitanda yace zikhale zasiliva.

11 Momwemonso pa mbali ya kumpoto m'utali mwace pakhale nsaru zocingira za mikono zana limodzi m'utali mwace; ndi nsici zace makumi awiri, ndi makamwa ao akhale amkuwa; zokowera za nsicizo ndi mitanda yace zikhale zasiliva.

12 Ndipo m'kupingasa kwa bwaloli pa mbali ya kumadzulo mukhale nsaru zocingira za mikono makumi asanu; nsici zace zikhale khumi, ndi makamwa ao khumi.

13 Ndipo m'kupingasa kwace kwa bwalo pa mbali ya kum'mawa, kum'mawa, mukhale mikono makumi asanu.

14 Ndi nsaru zocingira za pa mbali imodzi ya kucipata zikhale za mikono khumi ndi isanu; nsici zace zikhale zitatu, ndi makamwa ao atatu.

15 Ndi pa mbali yina pakhale nsaru zocingira za mikono khumi ndi isanu; nsici zace zikhale zitatu, ndi makamwa ao atatu.

16 Ndipo pa cipata ca bwalolo pakhale nsaru yotsekera ya mikono makumi awiri, ya lamadzi ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, nchito ya wopikula; nsici zace zikhale zinai, ndi makamwa ao anai.

17 Nsici zonse za pabwalo pozungulira zimangike pamodzi ndi mitanda yasiliva; zokowera zao zasiliva, ndi makamwa ao amkuwa.

18 Utali wace wa bwalolo ukhale wa mikono zana limodzi, ndi kupingasa kwace makumi asanu monsemo, ndi msinkhu wace wa mpanda mikono isanu; ukhale wabafuta wa thonje losansitsa; ndi makamwa a nsicizo akhale amkuwa.

19 Zipangizo zonse za kacisi, m'macitidwe ace onse, ndi ziciri zace zonse, ndi ziciri zonse za bwalo lace, zikhale zamkuwa.

Za mafuta a nyaliyo

20 Ndipo uuze ana a Israyeli akutengere mafuta a azitona oyera opera akuunikira, kuti awalitse nyali kosalekeza.

21 Aroni ndi ana ace aikonze m'cihema cokomanako, kunja kwa nsaru yocinga yokhala kumboni, kuyambira madzulo kufikira m'mawa; likhale lemba losatha mwa mibadwo yao, alisunge ana a Israyeli.