Eksodo 31 BL92

1 Za amisiri opanga nchitoyi, Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

2 Taona ndaitana ndi kumchula dzina lace, Bezaleli, mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa pfuke la Yuda;

3 ndipo ndamdzaza nd mzimu wa Mulungu, ndi luso, ndi nzeru, ndi cidziwitso, ndi m'nchito ziri zonse,

4 kulingirira nchito zaluso, kucita ndi golidi ndi siliva ndi mkuwa,

5 ndi kuzokota miyala yoikika, ndi kuzokota mtengo, kucita nchito ziri zonse.

6 Ndipo Ine, taona, ndampatsa Aholiabu, mwana wa Ahisama, wa pfuko la Dani, akhale naye; ndipo ndaika luso m'mitima ya onse a mtima waluso, kuti apange zonse ndakuuza iwe;

7 cihema cokomanako, likasa la mboni, ndi cotetezerapo ciri pamwamba pace, ndi zipangizo zonse za cihemaco;

8 ndi gomelo ndi zipangizo zace, ndi coikapo nyali coona ndi zipangizo zace, ndi guwa la nsembe lofukizapo;

9 ndi guwa la nsembe yopsereza ndi zipangizo zace zonse, ndi mkhate ndi tsinde lace;

10 ndi zobvala zotumikira nazo, ndi zobvala zopatulika za Aroni wansembe, ndi zobvala za ana ace, zakucita nazo nchito ya nsembe;

11 ndi mafuta odzoza, ndi cofukiza ca zonunkhira zokoma za malo opatulika; azicita monga mwa zonse ndakuuza iwe.

Masungidwe a dzuwa la Sabata

12 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

13 Koma iwe, lankhula ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Muzisunga masabata anga ndithu; pakuti ndiwo cizindikilo pakati pa Ine ndi inu mwa mibadwo yanu; kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova wakukupatulani.

14 Ndipo muzisunga Sabata; popeza ndilo lopatulika la kwa inu; ali yense wakuliipsa aphedwe ndithu; pakuti ali yense wakugwira nchito m'mwemo, munthu ameneyo asadzidwe mwa anthu a mtundu wace.

15 Agwire nchito masiku asanu ndi limodzi; koma lacisanu ndi ciwiri ndilo Sabata lakupumula, lopatulika la Yehova; ali yense wogwira nchito tsiku la Sabata aphedwe ndithu.

16 Cifukwa cace ana a Israyeli azisunga Sabata, kucita Sabata mwa mibadwo yao, likhale pangano losatha;

17 ndico cizindikilo cosatha pakati pa Ine ndi ana a Israyeli; pakuti Yehova analenga zam'mwamba ndi dziko lapansi masiku asanu ndi limodzi, napumula tsiku lacisanu ndi ciwiri, naonanso mphamvu.

18 Ndipo atatha iye kulankhula ndi Mose, pa phiri la Sinai, anampatsa magome awiri a mboni, magome amiyala, olembedwa ndi cala ca Mulungu.