1 Koma Mose analikuweta gulu la Yetero mpongozi wace, wansembe wa ku Midyani; natsogolera gululo m'tsogolo mwa cipululu, nafika ku phiri la Mulungu, ku Horebe.
2 Ndipo mthenga wa Molungu anamuonekera m'cirangali camoto coturuka m'kati mwa citsamba; ndipo anapenya, ndipo taonani, citsamba cirikuyaka moto, koma cosanyeka citsambaco.
3 Ndipo Mose anati, Ndipatuketu, ndikaone cooneka cacikuruco, citsambaco sicinyeka bwanji,
4 Pamene Yehova anaona kuti adapatuka kukapenya, Mulungu ali m'kati mwa citsamba, anamuitana, nati, Mose, Mose. Ndipo anati, Ndiri pano.
5 Ndipo iye anati, Usayandikire kuno; bvula nsapato zako ku mapazi ako, pakuti pamalo pamene upondapo iwe, mpopatulika.
6 Ananenanso Ine ndine Mulungu wa atate wako, Molungu wa Abrahamu, Molungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo. Ndipo Mose anabisa nkhope yace; popeza anaopa kuyang'ana Mulungu,
7 Ndipo Yehova anati, Ndapenyetsetsa mazunzo a anthu anga ali m'Aigupto, ndamvanso kulira kwao cifukwa ca akuwafulumiza; pakuti ndidziwa zowawitsa zao;
8 ndipo ndatsikira kuwalanditsa m'manja a anthu a Aigupto, ndi kuwatumtsa m'dziko lila akwere nalowe m'dziko labwino ndi lalikuru, m'dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi; ku malo a Akanani, ndi Ahiti ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi.
9 Ndipo tsopano, taona kulira kwa ana a Israyeli kwandifikira; ndapenyanso kupsinjika kumene Aaigupto awapsinja nako.
10 Tiye tsopano, ndikutuma kwa Farao, kuti uturutse anthu anga, ana a Israyeli m'Aigupto.
11 Koma Mose anati kwa Mulungu, Ndine yani ine kuti ndipite kwa Farao, ndi kuti nditurutse ana a Israyeli m'Aigupto?
12 Ndipo iye anati, Ine ndidzakhala ndi iwe; ndipo ici ndi cizindikilo ca iwe, cakuti ndakutuma ndine; utaturutsa anthuwo m'Aigupto mudzatumikira Mulungu paphiri pano.
13 Ndipo Mose anati kwa Mulungu, Onani, pakufika ine kwa ana a Israyeli, ndi kunena nao, Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu; ndipo akakanena ndi ine, Dzina lace ndani? ndikanena nao ciani?
14 Ndipo Molungu anati kwa Mose, INE NDINE YEMWE NDIRI INE. Anatinso, Ukatero ndi ana a Israyeli, INE NDINE wandituma kwa inu.
15 Ndipo Mulungu ananenanso kwa Mose, Ukatero ndi ana a Israyeli, Yehova, Molungu wa makolo anu, Molungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, ndi Molungu wa Yakobo anandituma kwa inu; ili nw dzina langa nthawi yosatha, ici ndi cikumbukiro canga m'mibadwo mibadwo.
16 Muka, nukasonkhanitse akuru a Israyeli, nunene nao, Yehova, Mulungu wa makolo anu anandionekera ine, Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Yakobo, ndi kuti; Ndakuzondani ndithu, ndi kuona comwe akucitirani m'Aigupto;
17 ndipo ndanena, Ndidzakukwezani kukuturutsani m'mazunzo a Aigupto, kukulowezani m'dziko la Akanani, ndi Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi, m'dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi.
18 Ndipo adzamveca mau ako; ndipo ukapite iwe ndi akuru a Israyeli, kwa mfumu ya Aigupto, ndi kukanena naye, Yehova, Mulungu wa Ahebri wakomana ndi ife; tiloleni, timuke tsopano ulendo wa masiku atatu m'cipululu, kuti timphere nsembe Yehova Mulungu wathu.
19 Koma Ine ndidziwa kuti mfumu ya Aigupto siidzalola inu kumuka, inde lingakhale ndi dzanja lamphamvu ai.
20 Ndipo ndidzatambasula dzanja langa, ndi kukantha Aigupto ndi zozizwa zanga zonse ndizicita pakati pace; ndi pambuyo pace adzakulolani kumuka.
21 Ndipo ndidzapatsa anthu awa ufulu pamaso pa anthu a Aigupto; ndipo kudzakhala, pamene muturuka simudzaturuka opanda kanthu;
22 koma mkazi yense adzafunse mnzace, ndi mlendo wokhala m'nyumba mwace, ampatse zokometsera zasiliva, ndi zokometsera zagolidi, ndi zobvala; ndipo mudzabveke nazo ana anu amuna ndi akazi; ndipo mudzafunkhe za Aaigupto.