1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi kuti,
2 Ndipatulire Ine yense woyamba kubadwa, wotsegulira pa amace mwa ana a Israyeli, mwa anthu ndi mwa zoweta; ndiwo anga.
3 Ndipo Mose ananena ndi anthu, Kumbukirani tsiku linu limene munaturuka m'Aigupto, m'nyumba ya akapolo; pakuti Yehova anakuturutsani muno ndi dzanja lamphamvu; ndipo asadye kanthu ka cotupitsa.
4 Muturuka lero lino mwezi wa Abibu.
5 Ndipo kudzakhala atakulowetsa Yehova m'dziko la Akanani, ndi la Ahiti, ndi la Aamori ndi la Ahivi, ndi la Ayebusi, limene analumbira ndi makolo ako kukupatsa, m'dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi, uzikasunga kutumikira kumeneku mwezi uno.
6 Masiku asanu ndi awiri uzikadya mkate wopanda cotupitsa, ndipo tsiku lacisanu ndi ciwiri likhale la madyerero a Yehova.
7 Azikadya mkate wopanda cotupitsa masiku asanu ndi awiriwo ndipo kasaoneke kanthu ka cotupitsa kwanu; inde cotupitsa cisaoneke kwanu m'malire ako onse.
8 Ndipo ukauze mwana wako wamwamuna tsikulo, ndi kuti, Nditero cifukwa comwe Yehova anandicitira ine poturuka ine m'Aigupto,
9 Ndipo cizikhala ndi iwe ngati cizindikilo pa dzanja lako, ndi cikumbutso pakati pa maso ako; kuti cilamulo ca Yehova cikhale m'kamwa mwako; pakuti Yehova anakuturutsa m'Aigupto ndi dzanja lamphamvu.
10 Cifukwa cace uzikasunga lemba ili pa nyengo yace caka ndi caka.
11 Ndipo kudzakhala, atakulowetsa Yehova m'dziko la Akanani, monga anakulumbirira iwe ndi makolo ako, ndipo anakupatsa ilo,
12 kuti uzikapatulira Yehova onse oyamba kubadwa ndi oyamba onse uli nao odzera kwa zoweta; amunawo ndi a Yehova.
13 Koma woyamba yense wa buru uzimuombola ndi mwana wa nkhosa; ndipo ukapanda kumuombola uzimthyola khosi; koma oyamba onse a munthu mwa ana ako uziwaombola.
14 Ndipo kudzakhala, akakufunsa mwana wako masiku akudzawo ndi kuti, Ici nciani? ukanene naye, Yehova anatiturutsa m'Aigupto, m'nyumba ya aka polo, ndi dzanja lamphamvu;
15 ndipo kunakhala, pamene Farao anadziumitsa kuti tisamuke, Yehova anawapha onse oyamba kubadwa m'dziko la Aigupto, kuyambira oyamba a anthu, kufikira oyamba a zoweta; cifukwa cace ndimphera nsembe Yehova zazimuna zoyamba kubadwa zonse; koma oyamba onse a ana anga ndiwaombola.
16 Ndipo cizikhala ngati cizindikilo pa dzanja lako, ndi capamphumi pakati pa maso ako; pakuti Yehova anatiturutsa m'Aigupto ndi dzanja lamphamvu.
17 Ndipo kunakhala pamene Farao adalola anthu amuke, Mulungu sanawatsogolera njira ya dziko la Afilisti, ndiyo yaifupi; pakuti Mulungu anati. Angadodome anthuwo pakuona nkhondo ndi kubwerera m'mbuyo kumka ku Aigupto.
18 Koma Mulungu anawazungulitsa anthuwo, ku njira ya kucipululu ya Nyanja Yofiira; ndipo ana a Israyeli anakwera kucokera m'dziko la Aigupto okonzeka.
19 Ndipo Mose anamuka nao mafupa a Yosefe; pakuti adawalumbiritsatu ana a Israyeli ndi kuti, Mulungu adzakuzondani ndithu ndipo mukakwere nao mafupa anga osawwya kuno.
20 Ndipo anacokera ku Sukoti, nagona ku Etamu, pa malekezero a cipululu.
21 Ndipo Yehova anawatsogolera usana ndi mtambo njo kuwatsogolera m'njira; ndi usiku ndi moto njo, wakuwawalitsira; kuti ayende usana ndi usiku;
22 sanacotsa mtambo usana, kapena mtambo wamoto usiku, pamaso pa anthu.