Eksodo 22 BL92

1 Munthu akaba ng'ombe, kapena nkhosa, nakaipha, kapena kuigulitsa, azilipa ng'ombe zisanu pa ng'ombeyo; ndi nkhosa zinai pa nkhosayo,

2 Akampeza wakuba alimkuboola, nakamkantha kotero kuti wafa, palibe camwazi.

3 Litamturukira dzuwa, pali camwazi; wakubayo azilipa ndithu; ngati alibe kanthu, amgulitse pa umbala wace.

4 Akacipeza cakubaco ciri m'dzanja lace camoyo, ngakhale ng'ombe, kapena buru, kapena nkhosa, alipe mowirikiza.

5 Munthu akadyetsa coweta pabusa kapena pa munda wamphesa, atamasula coweta cace, ndipo citadya podyetsa pa mwini wace; alipe podyetsa pace poposa, ndi munda wa mphesa wace woposa.

6 Ukayaka moto, nukalandira kuminga, kotero kuti unyeketsa mulu wa tirigu, kapena tirigu wosasenga, kapena munda; woyatsa motoyo alipe ndithu.

7 Munthu akaikiza ndalama kapena cuma kwa mnansi wace, ndipo zibeka m'nyumba ya munthuyo; akapeza mbala, ilipe cowirikiza.

8 Akapanda kumpeza mbalayo, abwere naye mwini nyumbayo kwa oweruza, kumuyesa ngati anaika dzanja lace pa cuma ca mnansi wace.

9 Mlandu uti wonse wa colakwa, kunena za ng'ombe, za buru, za nkhosa, za cobvala, za kanthu kali konse kotayika, munthu anenako kali kace; mlandu wa onse awiri ufike kwa oweruza; iye amene oweruza amtsutsa alipe cowirikiza kwa mnansi wace.

10 Munthu akaikiza buru, kapena ng'ombe, kapena nkhosa, kapena coweta cina kwa mnansi wace, ndipo cikafa, kapena ciphwetekwa, kapena wina acipitikitsa osaciona munthu;

11 lumbiro la Yehova likhale pakati pa iwo awiri, kuti sanaturutsa dzanja lace pa cuma ca mnansi wace; ndipo mwiniyo azibvomereza, ndipo asalipe.

12 Koma ngati cidabedwa kwaoko ndithu, alipe kwa mwiniyo.

13 Ngati cajiwa ndithu, abwere naco cikhale mboni; asalipe pa cojiwaco.

14 Munthu akabwereka cinthu kwa mnansi wace, ndipo ciphwetekwa, kapena cifa, mwiniyo palibe, azilipa ndithu.

15 Akakhalapo mwiniyo, asalipe; ngati cagwirira nchito yakulipira, cadzera kulipira kwace.

Malamulo osiyana a pakati pa anthu

16 Munthu akanyenga namwali wosapalidwa ubwenzi, nakagona nave, alipetu kuti akhale mkazi wace.

17 Atate wace akakana konse kumpatsa iye, alipe ndalama monga mwa colipa ca anamwali.

18 Wanyanga usamlola akhale ndi moyo.

19 Ali yense agona ndi coweta aphedwe ndithu.

20 Wakuphera nsembe mulungu wina, wosati Yehova yekha, aonongeke konse.

21 Ndipo usasautsa mlendo kapena kumpsinja; pakuti munali alendo m'dziko la Aigupto.

22 Musazunza mkazi wamasiye, kapena mwana wamasiye ali yense.

23 Ukawazunza ndi kakuti konse, nakandilirira pang'ono ponse iwowa, ndidzamvadi kulira kwao;

24 ndi mkwiyo wanga idzayaka, ndipo ndidzapha inu ndi lupanga; ndipo akazi anu adzakhala amasiye, ndi ana anu omwe.

25 Ukakongoletsa ndalama anthu anga osauka okhala nanu, usamkhalira ngati wangongole; usamwerengera phindu.

26 Ukati ulandire cikole kaya cobvala ca mnansi wako, koma polowa dzuwa ucibwezere kwa iye;

27 popeza copfunda cace ndi ici cokha, ndico cobvala ca pathupi pace; azipfundira ciani pogona? Ndipo kudzakhala kuti akandipfuulira Ine, ndidzamva; pakuti Ine ndine wacisomo.

28 Usapeputsa oweruza, kapena kutemberera mkuru wa anthu a mtundu wako.

29 Usacedwa kuperekako zipatso zako zocuruka, ndi zothira zako. Woyamba wa ana ako amuna undipatse Ine.

30 Uzitero nazo ng'ombe zako, ndi nkhosa zako; masiku asanu ndi atatu akhale ndi amai wace; tsiku lacisanu ndi citatu uzimpereka kwa Ine.

31 Ndipo muzindikhalira Ine anthu opatulika; cifukwa cace musamadya nyama yojiwa kuthengo; itayireni agaru.