1 Ndipo anacoka ku Elimu, ndi khamu lonse la ana a Israyeli linalowa m'cipululu ca Sini, ndico pakati pa Elimu ndi Sinai, tsiku lakhumi ndi cisanu la mwezi waciwiri ataturuka m'dziko la Aigupto.
2 Ndipo khamu lonse la ana a Israyeli linadandaulira Mose ndi Aroni m'cipululu;
3 nanena nao ana a Israyeli, Ha! mwenzi titafa ndi dzanja la Yehova m'dziko la Aigupto, pokhala ife pa miphika ya nyama, pakudya mkate ife cokhuta; pakuti mwatiturutsa kudza nafe m'cipululu muno kudzapha msonkhano uwu wonse ndi njala.
4 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ndidzabvumbitsira inu mkate wodzera kumwamba; ndipo anthu azituruka ndi kuola muyeso wa tsiku pa tsiku lace, kuti ndiwayese, ngati ayenda m'cilamulo canga kapena iai.
5 Ndipo kudzakhala tsiku lacisanu ndi cimodzi, kuti azikonza umene adabwera nao, ataoniezapo muyeso unzace wa pa tsiku limodzi.
6 Ndipo Mose ndi Aroni ananena ndi ana onse a Israyeli, Madzulo mudzadziwa kuti Yehova anakuturutsani m'dziko la Aigupto;
7 ndi m'mawa mwace mudzaona ulemerero wa Yehova, popeza alinkumva mulikudandaulira Yehova; pakuti ife ndife ciani, kuti mutidandaulira ife?
8 Nanenanso Mose, Pakukupatsani Yehova nyama ya kudya madzulo, ndi mkate wokhuta m'mawa, atero popeza Yehova adamva madandaulo anu amene mumdandaulira nao. Koma ife ndife ciani? simulikudandaulira ife koma Yehova.
9 Ndipo Mose anati kwa Aroni, Nena ndi khamu lonse la ana a Israyeli, Yandikizani pamaso pa Yehova, pakuti anamva madandaulo anu.
10 Ndipo kunakhala, pakunena Aroni ndi khamu lonse la ana a Israyeli kuti iwo anatembenukira kucipululu, ndipo, taonani, ulemerero wa Yehova unaoneka mumtambo.
11 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
12 Ndamva madandaulo a ana a Israyeli; lankhula nao ndi kuti, Madzulo mudzadya nyama, ndi m'mawa mudzakhuta mkate; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
13 Ndipo kunali madzulo zinakwera zinziri, ndipo zinakuta tsasa, ndi m'mawa padagwa mame pozungulira tsasa.
14 Ndipo atasansuka mame adagwawo, taonani, pankhope pa cipululu pali kanthu kakang'ono kamphumphu, kakang'ono ngati cipale panthaka.
15 Ndipo pamene ana a Israyeli anakaona, anati wina ndi mnzace, Nciani ici? pakuti sanadziwa ngati nciani. Ndipo Mose ananena nao, Ndiwo mkatewo Yehova wakupatsani ukhale cakudya canu,
16 Amenewo ndiwo mau walamulira Yehova, Aoleko yense monga mwa njala yace; munthu mmodzi omeri limodzi, monga momwe muli, yense atengere iwo m'hema mwace.
17 Ndipo ana a Israyeli anatero, naola wina wambiri, wina pang'ono.
18 Ndipo pamene anayesa ndi omeri, iye amene adaola wambiri sunamtsalira, ndi iye amene adaola pang'ono sunamsowa; yense anaola monga mwa njala yace.
19 Ndipo Mose ananena nao, Palibe munthu asiyeko kufikira m'mawa.
20 Koma sanammvera Mose; ndipo ena anasiyako kufikira m'mawa; koma unagwa mphutsi, nununkha. Ndipo Mose anakwiya nao.
21 Ndipo anauola m'mawa ndi m'mawa, yense monga mwa njala yace; popeza likatentha dzuwa umasungunuka.
22 Ndipo kunali tsiku lacisanu ndi cimodzi, anaola mkate, naonjezapo linzace, maomeri awiri pa munthu mmodzi; ndipo akazembe a khamulo anadza nauza Mose.
23 Ndipo ananena nao, Ici ndi comwe Yehova analankhula, Mawa ndiko kupuma, Sabata lopatulika la Yehova; cimene muzioca, ocani, ndi cimene muziphika phikani; ndi cotsala cikukhalireni cosunguka kufikira m'mawa.
24 Ndipo anausunga kufikira m'mawa, monga adalamulira Mose; koma sunanunkha, ndipo sunagwa mphutsi.
25 Ndipo Mose anati, Muudye lero; pakuti lero ndilo Sabata la Yehova; simuupeza lero pabwalo.
26 Muziola uwu masiku asanu ndi limodzi; koma tsiku lacisanu ndi ciwiri ndilo la Sabata, pamenepo padzakhala palibe.
27 Ndipo kunali tsiku la Sabata, kuti anthu ena anaturuka kukaola, koma sanaupeza.
28 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Mukana kusunga zouza zanga ndi malamulo anga kufikira titi?
29 Taonani, popeza Yehova anakupatsani Sabata, cifukwa cace tsiku lacisanu ndi cimodzi alikupatsa inu mkate wofikira masiku awiri; khalani yense m'malo mwace, munthu asaturuke m'malo mwace tsiku lacisanu ndi ciwiri.
30 Ndipo anthu anapumula tsiku lacisanu ndi ciwiri.
31 Ndipo mbumba ya Israyeli inaucha dzina lace Mana; ndiwo ngati zipatso zampasa, oyera; powalawa akunga timitanda tosanganiza ndi uci.
32 Ndipo Mose anati, Awa ndi mau anauza Yehova, Dzazani omeri nao, asungikire mibadwo yanu; kuti aone mkatewo ndinakudyetsani nao m'cipululu, muja ndinakuturutsani m'dziko la Aigupto.
33 Ndipo Mose anati kwa Aroni, Tenga mphika, nuthiremo mana odzala omeri, nuuike pamaso pa Yehova, usungikire mibadwo yanu.
34 Monga Yehova anauza Mose, momwemo Aroni anauika patsogolo pa Mboni, usungikeko.
35 Ndipo ana a Israyeli anadya mana zaka makumi anai, kufikira atalowa dziko la midzi; anadya mana kufikira analowa malire a dziko la Kanani.
36 Koma omeri ndilo limodzi la magawo khumi la efa.