Eksodo 18 BL92

Yetero azonda Mose nampangira

1 Ndipo Yetero, wansembe wa Midyani, mpongozi wa Mose, anamva zonse zimene Mulungu adacitira Mose ndi Israyeli anthu ace, kuti Yehova adaturutsa Israyeli m'Aigupto.

2 Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose, anabwera naye Zipora mkazi wa Mose (atamtuma kwao), ndi ana ace awiri;

3 dzina la winayo ndiye Gerisomu, pakuti anati, Ndakhala mlendo m'dziko lacilendo;

4 ndi dzina la mnzace ndiye Eliezere; pakuti anati, Mulungu wa kholo langa anakhala thandizo langa nandilanditsa ku lupanga la Farao.

5 Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose, anadza ndi ana ace amuna ndi mkazi wace kwa Mose kucipululu kumene adamangako, pa phiri la Mulungu;

6 nati kwa Mose, Ine mpongozi wako Yetero ndadza kwa iwe, ndi mkazi wako, ndi ana ace omwe awiri.

7 Ndipo Mose anaturuka kukakomana ndi mpongozi wace, nawerama, nampsompsona; nafunsana ali bwanji, nalowa m'hema.

8 Ndipo Mose anafotokozera mpongozi wace zonse Yehova adazicitira Farao ndi Aaigupto cifukwa ca Israyeli; ndi mabvuto onse anakomana nao panjira, ndi kuti Yehova adawalanditsa.

9 Ndipo Yetero anakondwera cifukwa ca zabwino zonse Yehova adazicitira Israyeli, ndi kuwalanditsa m'dzanja la Aaigupto.

10 Nati Yetero, Woyamikika Yehova, amene anakulanditsani m'dzanja la Aaigupto, ndi m'dzanja la Farao; ameneanalanditsa anthu awa pansi pa dzanja la Aaigupto.

11 Tsopano ndidziwa kuti Yehova ali wamkuru ndi milungu yonse; pakuti momwe anadzikuza okha momwemo anawaposa,

12 Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose, anamtengera Mulungu nsembe Yopsereza, ndi nsembe zophera; ndipo Aroni ndi akuru onse a Israyeli anadza kudzadya mkate ndi mpongozi wa Mose pamaso pa Mulungu.

13 Ndipo kunatero kuti m'mawa mwace Mose anakhala pansi kuweruzira anthu mirandu yao; ndipo anthu anakhala ciriri pamaso pa Mose kuyambira m'mawa kufikira madzulo.

14 Ndipo pamene mpongozi wace wa Mose anaona zonsezi iye anawacitira anthu, anati, Cinthu ici nciani uwacitira anthuci? Umakhala pa wekha bwanji, ndi anthu onse amakhala ciriri pamaso pako kuyambira m'mawa kufikira madzulo?

15 Ndipo Moce anati kwa mpongozi wace, Cifukwa anthu amadza kwa ine kudzafunsira Mulungu;

16 akakhala nao mlandu adza kwa ine, kuti ndiweruze pakati pa munthu ndi mnansi wace, ndi kuti ndiwadziwitsemalemba a Mulungu, ndi malamulo ace.

17 Koma mpongozi wa Mose ananena naye, Cinthu ucitaci siciri cabwino ai.

18 Udzalema konse, iwe ndi anthu amene uli nao; pakuti cikulaka cinthu ici; sungathe kucicita pa wekha.

19 Tamvera mau anga tsopano, ndikupangire nzeru, ndi Mulungu akhale nawe; ukhale m'malo mwa anthu kwa Mulungu, nupite nayo mirandu kwa Mulungu;

20 nuwamasulire malemba, ndi malamulo, ndi kuwadziwitsa njira imene ayenera kuyendamo, ndi nchito imene ayenera kucita.

21 Koma iwe, dzisankhire mwa anthu ako onse, amuna amtima, akuopa Mulungu, amuna oona, akudana nalo phindu la cinyengo; nuwaikire iwo oterewa, akuru a pa zikwi, akuru a pa mazana, akuru a pa makumi asanu, akuru a pa makumi;

22 ndipo iwo aweruze mirandu ya anthu nthawi zonse; ndipo kudzakhala kuti mirandu yaikuru yonse abwere nayo kwa iwe; koma mirandu yaing'ono yonse aweruze okha; potero idzakucepera nchito, ndi iwo adzasenza nawe.

23 Ukacite cinthuci, ndi Mulungu akakuuza cotero, udzakhoza kupirira, ndi anthu awa onse adzapita kwao mumtendere.

24 Ndipo Mose anamvera mau a mpongozi wace, nacita zonse adazinena.

25 Ndipo Mose anasankha amuna amtima mwa Aisrayeli onse, nawaika akuru a pa anthu, akuru a pa zikwi, akuru a pa mazana, akuru a pa makumi asanu, ndi akuru a pa makumi.

26 Ndipo anaweruza anthu nthawi zonse; mlandu wakuwalaka amabwera nao kwa Mose, ndi milandu yaing'ono yonse amaweruza okha.

27 Ndipo Mose analola mpongozi wace amuke; ndipo anacoka kumka ku dziko lace.