1 Ndipo Yehova ananena kwa Mose, Tsopano udzaona comwe ndidzacitira Farao; pakuti ndi dzanja lamphamvu adzawalola apite, inde ndi dzanja lamphamvu adzawaingitsa m'dziko lace.
2 Ndipo Mulungu ananena ndi Mose, nati kwa iye, Ine ndine YEHOV A:
3 ndipo ndinaonekera Abrahamu, Isake ndi Yakobo, Mulungu Wamphamvuyonse; koma sindinadziwika kwa iwo ndi dzina langa YEHOV A.
4 Ndipo ndinakhazikitsanso nao cipangano canga, kuwapatsa dziko la Kanani, dziko la maulendo ao, anali alendo m'mwemo.
5 Ndamvanso kubuula kwa ana a Israyeli, amene Aaigupto awayesa akapolo; ndipo ndakumbukila cipangano canga.
6 Cifukwa cace nena kwa ana a Israyeli, Ine ndine Yehova, ndipo ndidzakuturutsani pansi pa akatundu a Aaigupto, ndipo ndidzakulanditsani ku ukapolo wanu; ndipo ndidzakuombolani ndi dzanja lotambasuka, ndi maweruzo akuru;
7 ndipo ndidzalandira inu mukhale anthu anga, ndipo ndidzakhala Ine Mulungu wanu; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu, wakuturutsa inu pansi pa akatundu a Aaigupto.
8 Ndipo ndidzakulowetsani m'dziko limene ndinakweza dzanja langa kunena za ilo, kuti ndilipereke kwa Abrahamu, kwa Isake ndi kwa Yakobo; ndipo ndidzakupatsani ilo likhale lanulanu; Ine ndine Yehova.
9 Ndipo Mose ananena comweco ndi ana a Israyeli; koma sanamvera Mose cifukwa ca kuwawa mtima, ndi ukapolo wolemera.
10 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
11 Lowa, lankhula ndi Farao mfumu ya Aigupto, kuti alole ana a Israyeli aturuke m'dziko lace.
12 Koma Mose ananena pamaso pa Mulungu, ndi kuti, Onani, ana a Israyeli sanandimvera ine; adzandimvera bwanji Farao, ndine wa milomo yosadula?
13 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nawalangiza za ana a Israyeli, ndi za Farao mfumu ya Aigupto, kuti aturutse ana a Israyeli m'dziko la Aigupto.
14 Akuru a mbumba za makolo ao ndi awa: ana amuna a Rubeni, woyamba wa Israyeli ndiwo: Hanoki ndi Palu, Hezroni, ndi Karmi; amene ndiwo mabanja a Rubeni.
15 Ndi ana amuna a Simeoni ndiwo: Yemweli, ndi Yamini, ndi Ohadi, Yakini, ndi Zohari, ndi Sauli mwana wa mkazi wa m'Kanani; amene ndiwo mabanja a Simeoni.
16 Ndipo maina a ana amuna a Levi, mwa kubadwa kwao ndiwo: Gerisoni, ndi Kohati, ndi Merari; ndipo zaka za moyo wa Levi ndizo zana limodzi mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri.
17 Ana amuna a Gerisoni ndiwo: Libni ndi Simei, mwa mabanja ao.
18 Ndi ana amuna a Kohati ndiwo: Amramu ndi Izara, ndi Hebroni, ndi Uziyeli; ndipo zaka za moyo wa Kohati ndizo zana limodzi ndi makumi atatu kudza zitatu.
19 Ndipo ana amuna a Merai ndiwo: Mali ndi Musi. Amenewo ndiwo mabanja a Levi mwa kubadwa kwao.
20 Ndipo Amramu anadzitengera Yokobedi mlongo wa atate wace akhale mkazi wace; ndipo anambalira Aroni ndi Mose; ndi zaka za moyo wa Amramu ndizo zaria limodzi mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri.
21 Ndi ana amuna a lzara ndiwo: Kora: ndi Nefegi, ndi Zikiri.
22 Ndi ana amuna a Uziyeli ndiwo: Misayeli, ndi Elisafana, ndi Sitiri.
23 Ndipo Aroni anadzitengera Eliseba, mwana wamkazi wa Aminadabu, mlongo wace wa Nasoni, akhale mkazi wace; ndipo anambalira Nadabu ndi Abihu, Eleazara ndi ltamara.
24 Ndipo ana amuna a Kora ndiwo: Asiri ndi Elikana, ndi Abiasafu; amenewo ndiwo mabanja a Akora.
25 Ndipo Eleazara mwana wa Aroni anadzitengera mkazi wa ana akazi a Putieli akhale mkazi wace, ndipo anambalira Pinehasi. Amenewo ndi akuru a makolo a Alevi mwa mabanja ao.
26 Omwewo ndiwo Aroni ndi Mose amene Yehova ananena nao, Turutsani ana a Israyeli m'dziko la Aigupto mwa makamu ao.
27 Awa ndi omwewo ananena ndi Farao, mfumu ya Aigupto, awaturutse ana a Israyeli m'Aigupto; Mose ndi Aroni amenewa.
28 Ndipo kunali, tsiku limene Yehova ananena ndi Mose m'dziko la Aigupto,
29 Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Ine ndine Yehova: lankhula ndi Farao mfumu ya Aigupto zonsezi Ine ndizinena nawe.
30 Koma Mose anati pamaso pa Yehova, Onani, ine ndiri wa milome yosadula, ndipo Farao adzandimvera bwanji?