Eksodo 36 BL92

Pamenepo anacita Bezaleli ndi

1 Aholiabu, ndi anthu aluso, amene Yehova adaika luso ndi nzeru m'mtima mwao adziwe macitidwe ace a nchito yonse ya utumiki wace wa malo opatulika, monga mwa zonse adauza Yehova.

Amisiri alandira zopereka za anthu

2 Ndipo Mose adaitana Bezaleli ndi Aholiabu, ndi anthu onse aluso, amene Yehova adaika luso m'mtima mwao, onse ofulumidwa mtima ayandikize kunchito kuicita.

3 Ndipo analandira kwa Mose copereka conse, cimene ana a Israyeli adabwera naco cikhale ca macitidwe a nchito ya malo opatulika, aipange naco. Koma anaonjeza kubwera nazo kwa iye zopereka zofuna mwini, m'mawa ndi m'mawa.

4 Ndipo aluso onse, akucita nchito yonse ya malo opatulika, anadza onse ndi kusiya nchito yao: analinkucita;

5 nanena ndi Mose, ndi kuti, Anthu alinkubwera nazo zocuruka, zakuposera zoyenera nchito imene Yehova anauza icitike.

6 Ndipo Mose analamulira, ndipo anamveketsa mau mwa cigono conse, ndi kuti, Asaonjezere nchito ya ku copereka ca malo opatulika, ngakhale mwamuna ngakhale mkazi. Tero anawaletsa anthu asabwere nazo zina.

7 Popeza zipangizo zinakwanira nchito yonse icitike, zinatsalakonso.

Mapangidwe a cihemaco

8 Ndipo onse a mtima waluso mwa iwo akucita nchitoyi anapanga kacisi ndi nsaru zophimba khumi; anaziomba ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi lamadzi; ndi lofiira, ndi lofiira, ndi akerubi, nchito ya mmisiri.

9 Utali wace wa nsaru yophimba imodzi ndiwo mikono makumi awiri kudza isanu ndi itatu, ndi kupingasa kwace kwa nsaru imodzi mikono inai; nsaru zonse zinafanana muyeso wao.

10 Ndipo analumikiza nsaru zisanu yina ndi inzace; nalumikiza nsaru zisanu zina yina ndi inzace.

11 Ndipo anaika magango ansaru yamadzi m'mphepete mwace mwa nsaru imodzi ku mkawo wa cilumikizano; nacita momwemo m'mphepete mwace mwa nsaru ya kuthungo, ya cilumikizano caciwiri.

12 Anaika magango makumi asanu pa nsaru imodzi, naikanso magango makumi asanu m'mphepete mwace mwa nsaru ya cilumikizano cina; magango anakomanizana lina ndi linzace.

13 Ndipo anazipanga zokowera makumi asanu zagolidi, namanga nsaru pamodzi ndi zokowerazo; ndipo kacisi anakhala mmodzi.

14 Ndipo anaomba nsaru zophimba za ubweya wa mbuzi zikhale hema pamwamba pa kacisi; anaomba nsaru zophimba khumi ndi imodzi.

15 Utali wace wa nsaru imodzi ndiwo mikono makumi atatu, ndi kupingasa kwace kwa nsaru imodzi ndiko mikono inai; nsaru khumi ndi imodzi zinafanana muyeso wao.

16 Ndipo anamanga pamodzi nsaru zisanu pa zokha, ndi nsaru zisanu ndi imodzi pa zokha.

17 Ndipo anapanga magango makumi asanu m'mphepete mwa nsaru imodzi, ya kuthungo, ya cilumikizano, naika magango makumi asanu m'mphepete mwa nsaru ya kuthungo, ya cilumikizano cina.

18 Ndipo anapanga zokowera makumi asanu zamkuwa kumanga pamodzi hemalo, kuti likhale limodzi.

19 Ndipo anasokera hemalo cophimba ca zikopa za nkhosa zamphongo zonika zofiira, ndi cophimba ca zikopa za akatumbu pamwamba pace.

20 Ndipo anapanga matabwa a kacisi, oimirika, a mtengo wasitimu.

21 Utali wace wa thabwa limodzi ndiwo mikono khumi, ndi kupingasa kwace kwa thabwa limodzi ndiko mkono ndi hafu.

22 Pa thabwa limodzi panakhala mitsukwa iwiri, yomangika pamodzi; anawapanga momwemo matabwa onse a kacisi.

23 Ndipo anapanga matabwa a kacisi; matabwa makumi awiri a ku mbali ya kumwela, kumwela;

24 napanga makamwa makumi anai pansi pamatabwa makumi awiri; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi kwa mitsukwa yace iwiri, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina kwa mitsukwa yace iwiri.

25 Ndi ku mbali yina ya kacisi, mbali ya kumpoto, anapanga matabwa makumi awiri, ndi makamwa ao makumi anai asiliva;

26 makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina.

27 Ndi ku mbali ya kumbuyo ya kacisi kumadzulo anapanga matabwa asanu ndi limodzi.

28 Anapanganso matabwa awiri a ku ngondya za kacisi, m'mbali zace ziwirio

29 Ndipo anaphatikizika pamodzi patsinde, naphatikizilca pamodzi pamutu pace ndi mphete imodzi; anatero nao onse awiri pa ngondya ziwiri.

30 Ndipo panali matabwa asanu ndi atatu ndi makamwa ao asiliva, makamwa khumi kudza asanu ndi limodzi; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi.

31 Ndipo anapanga mitanda ya mtengo wasmmu; Isanu ya matabwa a pa mbali yina ya kacisi,

32 ndi mitanda isanu ya matabwa a pa mbali inzace ya kacisi, ndi mitanda lsanu ya matabwa a kacisi ali pa mbali ya kumadzulo.

33 Ndipo anapititsa mtanda wa pakatipo, pakati pa matabwa kufikira kuthungo.

34 Ndipo anakuta matabwa ndi golidi, napanga mphete zao zagolidi zikhale zopisamo mitandayo, nakuta mitandayo ndi golidi.

35 Ndipo anaomba nsaru yocinga ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa; anaciomba ndi akerubi nchito ya mmisiri.

36 Ndipo anaipangira mizati inai yasitimu, nazikuta ndi golidi; zokowera zao zinali zagolidi; ndipo anaziyengera makamwa anai asiliva.

37 Ndipo anaomba nsaru yotsekera pa khomo la cihemaco, ya lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, nchito ya wopikula;

38 ndi nsamamira zace zisanu ndi zokowera zao; nakuta mitu yao ndi mitanda yao ndi golidi; ndi makamwa ao asanu anali amkuwa.