Eksodo 8 BL92

Cozizwitsa caciwiri: Acule

1 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Lowa kwa Farao, nunene naye, Atero Yehova, Lola anthu anga amuke, kuti anditumikire.

2 Ndipo ukakana kuwalola amuke, taona, Ine ndidzapanda dziko lako lonse ndi acule;

3 ndipo m'nyanjamo mudzacuruka acule, amene adzakwera nadzalowa m'nyumba mwako, ndi m'cipinda cogona iwe, ndi pakama pako, ndi m'nyumba ya anyamata ako, ndi pa anthu ako, m'micembo yanu yooceramo, ndi m'mbale zanu zoumbiramo.

4 Ndipo acule adzakwera pa iwe, ndi pa anthu ako, ndi pa anyamata ako onse.

5 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Tambasula dzanja lako ndi ndodo yako, panyanja, pangalande, ndi pamatamanda, nukweretse acule pa dziko la Aigupto.

6 Ndipo Aroni anatambasula dzanja lace pa madzi a m'Aigupto; ndipo anakwera acule, nakuta dziko la Aigupto.

7 Ndipo alembi anacita momwemo ndi matsenga ao, nakweretsa acule pa dziko la Aigupto.

8 Pamenepo Farao anaitana Mose ndi Aroni, nati, Mundipembere Yehova, kuti andicotsere ine ndi anthu anga aculewo; ndipo ndidzalola anthu amuke, kuti amphere Yehova nsembe.

9 Koma Mose anati kwa Farao, Ulemu ndi wanu, wa ine ai; ndipembere inu ndi anyamata anu ndi anthu anu liti, kuti aonongeke aculewo, acokere inu ndi nyumba zanu, atsale m'nyanja mokha?

10 Ndipo anati, Mawa. Nati Mose, Kukhale monga mau anu, kuti mudziwe, kuti palibe wina wonga Yehova Mulungu wathu.

11 Ndipo acule adzacokera inu, ndi nyumba zanu, ndi anyamata anu, ndi anthu anu; adzatsala m'nyanja mokha.

12 Ndipo Mose ndi Aroni anaturuka kwa Farao; ndi Mose anapfuulira kwa Yehova kunena za acule amene adawaika pa Farao.

13 Ndipo Yehova anacita monga mwa mau a Mose; nafa aculewo kucokera m'zinyumba, ndi m'mabwalo, ndi m'minda.

14 Ndipo anawaola miulu-miulu; ndi dziko linanunkha.

15 Koma pamene Farao, anaona kuti panali kupuma, anaumitsa mtima wace, osamvera iwo; monga adalankhula Yehova.

Cozizwitsa cacitatu: Nsabwe

16 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Samula ndodo yako, nupande pfumbi lapansi, kuti lisanduke nsabwe m'dziko lonse la Aigupto.

17 Ndipo anacita comweco; pakuti Aroni anasamula dzanja lace ndi ndodo yace, napanda pfumbi lapansi, ndipo panali nsabwe pa anthu ndi pa zoweta; pfumbi lonse lapansi liinasanduka nsabwe m'dziko lonse la Aigupto.

18 Alembi anateronso ndi matsenga ao kuonetsa nsabwe, koma sanakhoza; ndipo panali nsabwe pa anthu, ndi pa zoweta.

19 Pamenepo alembi anati kwa Farao, Cala ca Mulungu ici; koma mtima wa Farao unalimba, osamvera iwo; monga adalankhula Yehova.

Cozozwitsa cacinai: Mizaza

20 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Uuke ulawire mamawa, nuime pamaso pa Farao; taona, aturuka kumka kumadzi; nunene naye, Atero Yehova, Lola anthu anga amuke, anditumikire.

21 Pakuti ukapanda kulola anthu anga amuke, taona, ndidzatuma mizaza pa iwe, ndi pa anyamata ako, ndi pa anthu ako, ndi pa nyumba zako; ndipo nyumba za Aaigupto zidzadzala nayo mizaza, ndi nthaka yomwe imene ikhalapo.

22 Ndipo tsiku ilo ndidzalemba malire dziko la Goseni, m'mene mukhala anthu anga, kuti pamenepo pasakhale mizaza; kotero kuti udziwe kuti Ine ndine Yehova pakati pa dzikoli.

23 Ndipo ndidzaika cosiyanitsa pakati pa anthu anga ndi anthu ako; mawa padzakhala cizindikilo ici.

24 Ndipo Yehovaanacita comweco; ndipo kunafika magulu a mizaza m'nyumba ya Farao, ndi m'nyumba za anyamata ace, ndi m'dziko lonse la Aigupto; dziko linaipatu cifukwa ca mizazayo.

25 Pamenepo Farao anaitana Mose ndi Aroni, nati, Mukani, mphereni nsembe Mulungu wanu m'dzikomu.

26 Koma Mose anati, Sikuyenera kutero; pakuti tidzamphera Yehova Mulungu wathu conyansa ca Aaigupto; taonani, ngati tikamphera nsembeconyansaca Aaigupto pamaso pao sadzatiponya miyala kodi?

27 Timuke ulendo wa masiku atatu m'cipululu, tikamphere Yehova Mulungu wathu nsembe, monga adzanena nafe.

28 Ndipo Farao anati, Ndidzakulolani mumuke, kuti mukamphere nsembe Yehova. Mulungu wanu m'cipululu; komatu musamuke kutaritu: mundipembere.

29 Ndipo Mose anati, Onani, ndirikuturuka ine kwanu, ndidzapemba Yehova kuti mizaza icoke mawa kwa Farao, ndi kwa anyamata ace, ndi kwa anthu ace; komatu, Farao asanyengenso ndi kukana kulola anthuwa amuke kukamphera nsembe Yehova.

30 Ndipo Mose anaturuka kwa Farao, napemba Yehova.

31 Ndipo Yehova anacita monga mwa mau a Mose; nacotsera Farao ndi anyamata ace ndi anthu ace mizazayo, sunatsala ndi umodzi wonse.

32 Koma Farao anaumitsa mtima wace nthawi yomweyonso, ndipo sanalola anthu amuke.