Eksodo 4 BL92

Mose alandira mphamvu yakucita zodabwiza

1 Ndipo Mose anayankha nati, Koma taonani, sadzakhulupirira ine, kapena kumvera mau anga; pakuti adzanena, Yehova sanakuonekera iwe.

2 Ndipo Yehova ananena naye, Ico nciani m'dzanja lako? Nati, Ndodo.

3 Ndipo ananena iye, Iponye pansi. Naiponya pansi, ndipo inasanduka njoka; ndipo Mose anaithawa.

4 Koma Yehova anati kwa Mose, Tambasula dzanja lako, nuigwire kumcira; ndipo anatambasula dzanja lace, naigwira, nikhalanso ndodo m'dzanja lace;

5 kuti akhulupirire kuti wakuonekera Yehova Mulungu wa makolo ao, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo.

6 Ndipo Yehova ananenanso naye, Longa dzanja lako pacifuwa pako. Ndipo analonga dzanja lace pacifuwa pace, naliturutsa, taonani, dzanja lace linali lakhate, lotuwa ngati cipale cofewa.

7 Ndipo ananena iye, Bwerezanso dzanja lako pacifuwa pako. Ndipo anabwerezanso dzanja lace pacifuwa pace; naliturutsa pacifuwa pace, taonani, linasandukanso lomwe lakale.

8 Ndipo kudzatero, ngati sakhulupirira iwe, ndi kusamvera mau a cizindikilo coyamba, adzakhulupirira mau a cizindikilo cotsirizaci.

9 Ndipo kudzatero, aka panda kukhulupirira zingakhale zizindikilo izi, ndi kusamvera mau ako, ukatunge madzi a kunyanja, ndi kuthira pamtunda; ndi madzi watunga ku nyanjayo adzasanduka mwazi pamtunda.

10 Ndipo Mose anati kwa Yehova, Mverani, Ambuye, ine ndine munthu wosowa ponena, kapena dzulo, kapena kale, kapena cilankhulire Inu ndi kapolo wanu, pakuti ndine wa m'kamwa molemera, ndi wa lilime lolemera.

11 Koma Yehova ananena naye, Anampangira munthu m'kamwa ndani? Kapena analenga munthu wosalankhula ndani, kapena wogontha, kapena wamaso, kapena wakhungu? Si ndine Yehova kodi?

12 Ndipo tsopano muka, ndipo Ine ndidzakhala m'kamwa mwako, ndi kukuphunzitsa comwe ukalankhule.

13 Koma anati, Mverani, Ambuye, tumizani pa dzanja la iye amene mudzamtuma.

14 Pamenepo mkwiyo wa Yehova unamyakira Mose, ndipo anati, Nanga Aroni Mlevi mbale wako sialipo kodi? Ndidziwa kuti kulankhula alankhula. Ndipo, taona, aturuka kudzakomana ndiwe; ndipo pakuona iwe adzakondweram'mtima mwace.

15 Ndipo ukalankhule naye, ndi kumpangira mau; ndipo Ine ndidzakhala m'kamwa mwako, ndi m'kamwa mwace, ndipo ndidzakuphunzitsani inu cimene mukacite.

16 Ndipo iye adzakulankhulira iwe kwa anthu; ndipo kudzatero, kuti iye adzakhala kwa iwe ngati m'kamwa, ndi iwe udzakhala kwa iye ngati Mulungu.

17 Ndipo ukaigwire m'dzanja lako ndodo iyi, imene ukacite nayo zizindikilozo.

18 Ndipo Mose anabwera namuka kwa Yetero mpongozi wace, nanena naye, Ndimuketu, ndibwerere kumka kwa abale anga amene ali m'Aigupto, ndikaone ngati akali ndi moyo. Ndipo Yetero ananena ndi Mose, Pita bwino.

19 Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'Midyani, Muka, bwerera kumka ku Aigupto; pakuti adafa anthu onse amene anafuna moyo wako.

20 Pamenepo Mose anatenga mkazi wace ndi ana ace amuna, nawakweza pa buru, nabwerera kumka ku dziko la Aigupto; ndipo Mose anagwira ndodo ya Mulungu m'dzanja lace.

21 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Pakumuka iwe kubwerera kumka ku Aigupto, usamalire ucite zozizwa zonse ndaziika m'dzanja lako, pamaso pa Farao; koma Ine ndidzalimbitsa mtima wace kuti asadzalole anthu kupita.

22 Pamenepo ukanene ndi Farao, Atero Yehova, Mwana wanga, mwana wanga woyamba ndiye Israyeli.

23 Ndipo ndanena ndi iwe, Mlole mwana wanga amuke, kuti anditumikire Ine; koma wakana kumlola kuti asamuke; taona, Ine ndidzamupha mwana wako wamwamuna, mwana wako woyamba.

24 Ndipo kunali panjira, kucigono, Yehova anakomana naye, nafuna kumupha.

25 Koma Zipora anatenga mpeni wamwala, nadula khungu la mwana wace, naliponya pa mapazi ace; nati, Pakuti iwe ndiwe mkwati wanga wamwazi. Ndipo iye anamleka.

26 Pamenepo anati mkaziyo, Mkwati wamwazi iwe, cifukwa ca mdulidwe.

Mose akomana ndi Aroni

27 Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Muka kucipululu kukakomana ndi Mose. Ndipo anamuka, nakomana naye pa phiri la Mulungu, nampsompsona.

28 Ndipo Mose anauza Aroni mau onse a Yehova amene adamtuma nao, ndi zizindikilo zonse zimene adamlamulira.

29 Pamenepo Mose ndi Aroni anamuka nasonkhanitsa akuru onse a ana a Israyeli;

30 ndipo Aroni anawafotokozera mau onse amene Yehova adauza Mose, nacita zizindikilo zija pamaso pa anthu.

31 Ndipo anthuwo anakhulupirira; ndipo pamene anamva kuti Yehova adawazonda ana a Israyeli, ndi kuti adaona mazunzo ao, anawerama, nalambira Mulungu.