Eksodo 11 BL92

Cozizwitsa cakhumi: Imfa ya ana oyamba kubadwa

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Watsala moo umodzi ndidzamtengera Farao, ndi Aigupto; pambuyo pace adzakulolani mucoke kuno; pamene akulolani kupita, zoonadi adzakuingitsani kuno konse.

2 Lankhula tsopano m'makutu a anthu, kuti mwamuna yense apemphe kwa mnzace, ndi mkazi yense kwa mnzace, zokometsera zasiliva ndi zagolidi.

3 Ndipo Yehova anawapatsa anthu cisomo pamaso pa Aaigupto. Munthuyo Mose ndiyenso wamkuru ndithu m'dziko la Aigupto, pamaso pa anyamata a Farao, ndi pamaso pa anthu.

4 Ndipo Mose anati, Atero Yehova, Monga pakati pa usiku ndidzaturuka loe kumka pakati pa Aigupto;

5 ndipo ana onse oyamba a m'dziko la Aigupto adzafa, kuyambira mwana woyamba wa Farao wokhala pa mpando wacifumu wace, kufikira mwana woyamba wa mdzakazi wokhala pa miyala yopera; ndi ana onse oyamba a zoweta.

6 Ndipo kudzakhala kulira kwakukuru m'dziko lonse la Aigupto, kunalibe kunzace kotere, sikudzakhalanso kunzace kotere.

7 Koma palibe garu adzafunyitsira lilime lace ana onse a Israyeli ngakhale anthu kapena zoweta; kuti mudziwe kuti Yehova asiyanitsa pakati pa Aaigupto ndi Aisrayeli.

8 Ndipo anyamata ako onse awa adzanditsikira, nadzandigwadira, ndi kuti, Turukani inu, ndi anthu onse akukutsatani; ndipo pambuyo pace ndidzaturuka. Ndipo anaturuka kwa Farao wakupsa mtima.

9 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Farao sadzamvera inu; kuti zozizwa zanga zicuruke m'dziko la Aigupto.

10 Ndipo Mose ndi Aroni anacita zozizwa izi zonse pamaso pa Farao; koma Yehova analimbitsa mtima wace wa Farao, ndipo sanalola ana a Israyeli aturuke m'dziko lace.