1 Koma pamene anaona kuti Mose anacedwa kutsika m'phiri, anthuwo anasonkhana kwa Aroni, nanena naye, Ukani, tipangireni milungu yakutitsogolera; pakuti Mose uyu, munthuyu anatikweza kucokera m'dziko la Aigupto, sitidziwa comwe camgwera.
2 Ndipo Aroni ananena nao, Thyolani mphete zagolidi ziri; m'makutu a akazi anu, a ana anu amuna ndi akazi, ndi kubwera nazo kwa ine.
3 Ndipo anthu onse anathyola mphete zagolidi zinali m'makutu mwao, nabwera nazo kwa Aroni.
4 Ndipo anazilandira ku manja ao, nacikonza ndi cozokotera, naciyenga mwana wa ng'ombe; ndipo anati, Siyi milungu yako, Israyeli, imene inakukweza kucokera m'dziko la Aigupto.
5 Pakuciona Aroni, anamanga guwa la nsembe patsogolo pace; ndipo Aroni anapfuula nati, Mawa aliko madyerero a Yehova.
6 Ndipo m'mawa mwace anauka mamawa, nafukiza nsembe zopsereza, nabwera nazo nsembe zamtendere; ndi anthu anakhala pansi kudya ndi kumwa, nauka kusewera.
7 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka, tsikatu, pakuti anthu ako udakwera nao kucokera m'dziko la Aigupto wadziipsa;
8 wapatuka msanga njira imene ndinawauza; wadzinyengera mwana wa ng'ombe, namgwadira, namphera nsembe, nati, Siyi milungu yako, Israyeli, imene inakukweza kucokera m'dziko la Aigupto,
9 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ndawapenya anthu awa, taona, ndiwo anthu opulupudza;
10 ndipo tsopano ndileke, kuti ndipse mtima pa awo ndi kuwatha, ndi kukuza iwe ukhale mtundu waukuru.
11 Ndipo Mose anapemba kwa Yehova Mulungu wace, nati, Yehova, mtima wanu upserenji pa anthu anu, amene munawaturutsa m'dziko la Aigupto ndi mphamvu yaikuru, ndi dzanja lolimba?
12 Akaneneranji Aaigupto; ndi kuti, Anawaturutsa coipa, kuti awaphe m'mapiri, ndi kuwatha pankhope pa dziko lapansi? Pepani, lekani coipaco ca pa anthu anu.
13 Kumbukilani Abrahamu, Isake ndi Israyeli, atumiki anu, amene munawalumbirira ndi kudzichula nokha, amene munanena nao, Ndidzacurukitsa mbeu zanu ngati nyenyezi za kuthambo, ndi dziko ili lonse ndanenali ndidzapatsa mbeu zanu, likhale colowa cao nthawi zonse.
14 Ndipo Yehova analeka coipa adanenaci, kuwacitira anthu ace.
15 Ndipo Mose anatembenuka, natsika m'phirimo, magome awiri a mboni ali m'dzanja lace; magome olembedwa kwina ndi kwina; analembedwa mbali yina ndi inzace yomwe.
16 Ndipo magomewo ndiwo nchito ya Mulungu, kulembaku ndiko kulemba kwa Mulungu, kozokoteka pa magomewo.
17 Ndipo pamene Yoswa anamva phokoso la kupfuula kwa anthu, anati kwa Mose, Kuli phokoso la nkhondo kucigono.
18 Koma iye anati, Phokosoli sindilo la kupfuula kwa olakika, kapena la kupfuula kwa opasuka; koma phokoso ndikumvali ndilo la othirirana mang'ombe.
19 Ndipo kunali, pamene anayandikiza cigono, anaona mwana wa ng'ombeyo ndi kubvinako; ndipo Mose anapsa mtima, nataya magome ali m'manja mwace, nawaswa m'tsinde mwa phiri.
20 Ndipo anatenga mwana wa ng'ombe anampangayo, namtentha ndi moto, nampera asalale, namwaza pamadzi, namwetsako ana a Israyeli.
21 Ndipo Mose anati kwa Aroni, Anthu awa anakucitiranji, kuti iwe watengera iwo kulakwa kwakukuru kotere?
22 Ndipo Aroni anati, Asapse mtima mbuye wanga; udziwa anthuwa kuti akhumba coipa.
23 Pakuti ananena nane, Tipangireni milungu yakutitsogolera; popeza Mose uyu, munthuyu anatikweza kucokera m'dziko la Aigupto, sitidziwa comwe camgwera.
24 Ndipo ndinanena nao, Ali yense ali naye golidi amthyole; ndipo anandipatsa; ndipo ndinaciponya m'moto, ndimo anaturukamo mwana wa ng'ombe uyu.
25 Ndipo pamene Mose anaona kuti anthu anamasuka, popeza Aroni adawamasula kuti awatonze adani ao,
26 Mose anaima pa cipata ca cigono, nati, Onse akubvomereza Yehova, adze kwa ine. Pamenepo ana amuna onse a Levi anasonkhana kwa iye,
27 Ndipo ananena nao, Atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Yense amange lupanga lace m'cuuno mwace, napite, nabwerere kuyambira cipata kufikira cipata, pakati pa cigono, naphe yense mbale wace, ndi yense bwenzi lace, ndi yense mnansi wace.
28 Ndipo ana a Levi anacita monga mwa mau a Mose; ndipo adagwa tsiku lija anthu ngati zikwi zitatu.
29 Popeza Mose adati, Mdzazireni Yehova manja anu lero, pakuti yense akhale mdani wa mwana wace wamwamuna, ndi mdani wa mbale wace; kuti akudalitseni lero lino.
30 Ndipo kunali m'mawa mwace, kuti Mose anati kwa anthu, Mwacimwa kucimwa kwakukulu; koma ndikwera kwa Yehova tsopano, kapena ndidzacita cotetezera ucimo wanu.
31 Ndipo Mose anabwerera kumka kwa Yehova, nati, Ha! pepani, anthu awa anacimwa kucimwa kwakukuru, nadzipangira milungu yagolidi.
32 Koma tsopano, kapena mudzakhululukira kucimwa kwao; koma ngati mukana, mundifafanizetu, kundicotsa m'buku lanu limene munalembera,
33 Ndipo Yehova anati kwa Mose, iye amene wandicimwira, ndifafaniza yemweyo kumcotsa m'buku langa.
34 Ndipo tsopano, muka, tsogolera anthu kumka nao kumene ndinakuuza; taona, mthenga wanga akutsogolera; koma tsiku lakuwazonda Ine ndidzawalanga cifukwa ca kucimwa kwao.
35 Ndipo Yehova anakantha anthu, cifukwa anapanga mwana wa ng'ombe amene Aroni anapanga.