1 Ndipo upange guwa la nsembe la kufukizapo; ulipange la mtengo wasitimu.
2 Utali wace ukhale mkono, ndi kupingasa kwace mkono; likhale lampwamphwa; ndi msinkhu wace mikono iwiri; nyanga zace zituruke m'mwemo.
3 Ndipo ulikute ndi golidi woona, pamwamba pace ndi mbali zace zozungulira, ndi nyanga zace; ulipangirenso mkombero wagolidi pozungulira,
4 Ndipo ulipangire mphete ziwiri zagolidi pansi pa mkombero wace; uziike pa nthiti zace ziwiri, pa mbali zace ziwiri; zikhale zopisamo mphiko kulinyamula nazo.
5 Ndipo upange mphiko za mtengo wasitimu, ndi kuzikuta ndi golidi.
6 Nuliike cakuno ca nsaru yocinga iri ku likasa la mboni, patsogolo pa cotetezerapo ciri pamwamba pa mboni, pomwe ndidzakomana ndi iwe.
7 Ndipo Aroni azifukizapo cofukiza ca zonunkhira zokoma m'mawandim'mawa, pamene akonza nyalizo, acifukize.
8 Ndipo pamene Aroni ayatsa nyalizo madzulo, acifukize cofukiza cosatha pamaso pa Yehova mwa mibadwo yanu,
9 Musafukizapo cofukiza cacilendo, kapena nsembe yopsereza, kapena copereka; musathirepo nsembe yothira.
10 Ndipo Aroni azicita coteteza pa nyanga zace kamodzi m'caka; alicitire coteteza ndi mwazi wa nsembe yaucimo ya coteteza, mwa mibadwo yanu; ndilo lopatulikitsa la Yehova.
11 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
12 Pamene uwerenga ana a Israyeli, monga mwa mawerengedwe ao, munthu yense apereke kwa Yehova ciombolo ca pa moyo wace, pa kuwerengedwa iwowa; kuti pasakhale mliri pakati pao, pakuwerengedwa iwowa.
13 Ici acipereke, yense wakupita kwa owerengedwa; limodzi la magawo awiri a sekeli, monga sekeli la malo opatulika; (sekeli ndilo magera makumi awiri) limodzi la magawo awiri a sekeli, ndilo copereka ca Yehova.
14 Yense wakupita kwa owerengedwawo, wa zaka makumi awiri ndi wa mphambu zace, apereke coperekaco kwa Yehova.
15 Wacuma asacurukitsepo, ndi osauka asacepse pa limodzi mwa magawo awiri a sekeli, pakupereka copereka kwa Yehova, kucita coteteza ca miyoyo yanu.
16 Ndipo uzilandira ndarama za coteteza kwa ana a Israyeli, ndi kuzipereka pa nchito ya cihema cokomanako; kuti zikhale cikumbutso ca ana a Israyeli pamaso pa Yehova, kucita coteteza ca miyoyo yanu.
17 Ndipo Yehova analankhula ndi Mose, ndi kuti,
18 Upangenso mkhate wamkuwa, ndi tsinde lace lamkuwa, wakusambiramo; nuuike pakati pa ciliema cokomanako ndi guwa la nsembe, ndi kuthiramo madzi.
19 Ndipo Aroni ndi ana ace amuna azisambiramo manja ao ndi mapazi ao;
20 pakulowa iwo m'cihema cokomanako asambe ndi madzi, kuti angafe; kapena poyandikiza guwa la nsembe kutumikirako, kufukiza nsembe yamoto ya Yehova;
21 asambe manja ao ndi mapazi ao, kuti angafe: liwakhalire lemba losatha, kwa iye ndi kwa mbeu zace, mwa mibadwo yao.
22 Yehova ananenanso ndi Mose, ndi kuti,
23 Udzitengerenso zonunkhira zomveka, mure woyenda masekeli mazana asanu, ndi kinimani lonunkhira limodzi mwa magawo awiri a mureyo, ndilo masekeli mazana awiri kudza makumi asanu, ndi kane lonunkhira mazana awiri kudza makumi asanu,
24 ndi kida mazana asanu, monga sekeli la malo opatulika, ndi mafuta a azitona hini limodzi;
25 ndipo ukonze nazo mafuta odzoza opatulika, osanganizika monga mwa macitidwe a wosanganiza; akhale mafuta odzoza opatulika.
26 Ndipo udzoze nao cihema cokomanako, ndi likasa la mboni,
27 ndi gomelo ndi zipangizo zace zonse, ndi coikapo nyali ndi zipangizo zace,
28 ndi guwa la nsembe lofukizapo, ndi guwa la nsembe yopsereza ndi zipangizo zace zonse, ndi mkhate wosambiramo ndi tsinde lace.
29 Ndipo uzipatule, kuti zikhale zopatulika ndithu; zonse zakuzikhudza zidzakhala zopatulika.
30 Ndipo udzoze Aroni ndi ana ace amuna, ndi kuwapatula andicitire nchito ya nsembe.
31 Nulankhule ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Awa ndi mafuta odzoza opatulika a Ine mwa mibadwo yanu.
32 Asawatsanulire pa thupi la munthu; kapena musakonza ena onga awa, mwa makonzedwe ace; awa ndiwo opatulika, muwayese opatulika.
33 Ali yense amene akonza ena otere, kapena ali yense awaika pa mlendo, ameneyo asazidwe kwa anthu a mtundu wace.
34 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Udzitengere zonunkhira, natafi, ndi sekeleti, ndi kelebuna; zonunkhira pamodzi ndi libano loona; miyeso yofanana;
35 ndipo uzikonza nazo cofukiza, cosanganiza mwa macitidwe a wosanganiza, cokometsera ndi mcere, coona, copatulika;
36 nupere cina cisalale, nuciike cakuno ca mboni m'cihema cokomanako, kumene ndidzakomana ndi iwe; uciyese copatulika ndithu.
37 Koma za cofukizaco ucikonze, musadzikonzere nokha cina, mwa makonzedwe ace amene; muciyese copatulika ca Yehova.
38 Ali yense wokonza cina cotere kununkhizapo, asadzidwe kwa anthu a mtundu wace.