Eksodo 28 BL92

Za zobvala zopatulika

1 Ndipo akuyandikire Aroni mbale wako, ndi ana ace amuna pamodzi naye, mwa ana a Israyeli, kuti andicitire Ine nchito ya nsembe, ndiwo Aroni, Nadabu, ndi Abihu, Eleazara ndi ltamara, ana a Aroni.

2 Ndipo usokere Aroni mbale wako zobvala zopatulika, zikhale zaulemerero ndi zokoma.

3 Ndipou lankhule ndi onse a mtima waluso, amene ndawadzaza ndi mzimu waluso, kuti amsokere Aroni zobvala apatulidwe nazo, andicitire Ine nchito ya nsembe.

4 Ndipo zobvala azisoka ndizi: capacifuwa ndi efodi, ndi mwinjiro, ndi malaya opikapika, ndi nduwira, ndi mpango; tero apangire Aroni mbale wako ndi ana ace zobvala zopatulika, kuti andicitire Ine nchito ya nsembe,

5 Ndipo atenge golidi, ndi lamadzi ndi lofiirira ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.

Za Efodi

6 Naombe efodi ndi golidi, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira ndi bafuta wa thonje losansitsa, nchito ya mmisiri.

7 Akhale nazo zapamapewa ziwiri zomangika ku nsonga zace ziwiri, kuti amangike nazo.

8 Ndipo mpango wa efodi, wokhala pamenepo, kuti ammange nao, ukhale wa ciombedwe comweco, ndi woombera kumodzi, wagolidi, ndi thonje lamadzi, ndi lofiirira ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.

9 Ndipo utenge miyala iwiri yaberulo, nulocepo maina a ana a Israyeli;

10 maina asanu ndi limodzi pa mwala wina, ndi maina asanu ndi limodzi otsala pa mwala unzace, mwa kubadwa kwao.

11 Uloce miyala iwiriyo ndi maina a ana a Israyeli, monga mwa nchito ya woloca miyala, monga malembedwe a cosindikizira, uipange igwirike ndi zoikamo zagolidi,

12 Ndipo ulike miyala iwiriyo pa zapamapewa za efodi, ikhale miyala ya cikumbutso ca ana a Israyeli; ndipo Aroni azinyamula maina ao pa mapewa ace awiri, akhale cikumbutso pamaso pa Yehova.

13 Ndipo upange zoikamo za golidi;

14 ndi maunyolo awiri a golidi woona; uwapote ngati zingwe, nchito yopota; numange maunyolo opotawo pazoikamo.

15 Upangenso capacifuwa ca ciweruzo, nchito ya mmisiri; uciombe mwa ciombedwe ca efodi; uciombe ndi golidi, lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.

16 Cikhale campwamphwa, copindika, utali wace cikhato cimodzi, ndi kupingasa kwace cikhato cimodzi.

17 Ndipo uikepo miyala yoikikapo, mizere inai ya miyala; mzere wa odemu, pitida, ndi bareketi, ndiyo ya mzere woyamba;

18 ndi mzere waciwiri wa nofeki, safiri, ndi yahaloni;

19 ndi mizere wacitatu wa lesemu, sibu, ndi akalama;

20 ndi mzere wacinai wa tarisisi, sohamu, ndi yasefe; zikhale zogwirika ndi golidi m'zoikamo zao.

21 Ndi miyalayi ikhale monga mwa maina a ana a Israyeli, khumindiawiri, monga maina ao; monga malocedwe a cosindikizira, yonse ikhale monga maina ao, kwa mafuko khumi ndi awiri.

22 Upangenso maunyolo pa capacifuwa ngati zingwe, nchito yopota, ya golidi woona.

23 Nupangire pa capacifuwa mphete ziwiri zagolidi, ndi kuzika mphete ziwirizo pa nsonga zace ziwiri za capacifuwa.

24 Numange maunyolo awiri opota agolidi ku mphete ziwiri pansonga pace pa capacifuwa.

25 Koma nsonga zace ziwiri za maunyolo opotawo uzimange ku zoikamo ziwiri, ndi kuziika pa zapamapewa ziwiri za efodi, m'tsogolo mwace.

26 Ndipo upange mphete ziwiri zagolidi, ndi kuzimanga pa nsonga zace ziwiri za capacifuwa, m'mphepete mwace, m katimo ku mbali ya kuefodi.

27 Upangenso mphete ziwiri zagolidi, ndi kuzimanga pa zapamapewa ziwiri za efodi, m'munsi, ku mbali yace ya kutsogolo, pafupi pa msoko wace, pamwamba pa mpango wa efodi.

28 Ndipo amange capacifuwa pa mphete zace ndi mphete za efodi ndi mkuzi wamadzi, kuti cikhale pa mpango wa efodi; ndi kuti capacifuwa cisamasuke paefodi,

29 Ndipo Aroni azinyamula maina a ana a Israyeli pa capacifuwa ca ciweruzo pamtima pace, pakulowa iye m'malo opatulika, akhale cikumbutso pankhope pa Yehova kosalekeza.

30 Ndipo uike Urimu ndi Tumimu mwa capacifuwa ca ciweruzo; ndipo zikhale pa mtima wa Aroni, pakulowa iye pamaso pa Yehova; ndipo Aroni azinyamula ciweruzo ca ana a Israyeli pamtima pace pamaso pa Yehova kosalekeza.

31 Ndipo uombe mwinjiro wa efodi ndi lamadzi lokha.

32 Ndipo polowa mutu pakhale pakati pace; pakhale mkawo pozungulira polowa pace, wa nchito yoomba, ngati polowa pa malaya ociniiriza, pangang'ambike.

33 Ndipo pa mbinyiru wace upange makangaza a lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiirira, pambinyiru pace pozungulira, ndi kuwapakiza ndi miliu yagolidi pozungulira;

34 mliu wagolidi ndi khangaza, mliu wagolidi ndi khangaza, pa mbinyiru wa mwinjiro pozungulira.

35 Ndipo Aroni aubvale kuti atumikire nao; ndipo limveke liu lace pakulowa iye m'malo opatulika pamaso pa Yehova, ndi pakuturuka iye, kuti asafe.

Za golidi waphanthiphanthi

36 Ndipo upange golidi waphanthiphanthi woona, ndi kulocapo, monga malocedwe a cosindikizira. KUPATULIKIRA YEHOVA.

37 Nuciike pamkuzi wamadzi, ndipo cikhale panduwira, cikhale patsogolo pace pa nduwira.

38 Ndipo cizikhala pamphumi pace pa Aroni, ndipo Aroni azinyamula mphulupulu ya zopatulidwa, zimene ana a Israyeli azipatulira, ndi zopereka zao zonse zopatulira; ndipo cizikhala pamphumi pace kosalekeza, kuti alandiridwe pamaso pa Yehova.

39 Ndipo upikule maraya am'kati abafuta a thonje losansitsa, nusoke nduwira wabafuta, nusokenso mpango wopikapika.

40 Ndipo usokere ana a Aroni maraya am'kati, nuwasokere mipango; uwasokerenso akapa akhale aulemerero ndi okoma.

41 Ndipo ubveke nazo Aroni mbale wako, ndi ana ace omwe; ndi a kuwadzoza, ndi kudzaza dzanja lao, ndi kuwapatula, andicitire Ine nchito ya nsembe.

42 Uwasokerenso zobvala za miyendo za bafuta wa thome losansitsa kubisa marisece ao; ziyambire m'cuuno zifikire kuncafu.

43 Ndipo azibvale Aroni, ndi ana ace, pakulowa iwo ku cihema cokomanako, kapena poyandikiza iwo ku guwa la nsembe kutumikira m'malo opatulika; anganyamule mphulupulu, nangafe; likhale lemba losatha la iye ndi mbumba zace pambuyo pace.